Yobu 1:1-22

1  Kudziko la Uzi+ kunali munthu wina dzina lake Yobu.+ Iye anali munthu wopanda cholakwa,+ wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndiponso wopewa zoipa.+  Yobu anali ndi ana aamuna 7, ndi ana aakazi atatu.+  Iye anali ndi ziweto+ izi: Nkhosa 7,000, ngamila 3,000, ng’ombe 1,000 zomwe zinali kugwira ntchito zili ziwiriziwiri, ndi abulu aakazi 500. Analinso ndi antchito ochuluka zedi, ndipo iye anali munthu wolemekezeka kwambiri pa anthu onse a Kum’mawa.+  Ana ake aamuna anali kuchita phwando+ kunyumba ya aliyense wa iwo, tsiku lina kwa wina, tsiku lina kwa wina, ndipo anali kuitana alongo awo atatu kuti adzadye ndi kumwera limodzi.  Akamaliza kuchita maphwando kunyumba zawo zonse, Yobu anali kutumiza uthenga n’kuwauza kuti adziyeretse.+ Kenako iye anali kudzuka m’mawa kwambiri n’kupereka nsembe zopsereza+ mogwirizana ndi chiwerengero cha ana ake onse, popeza iye ankati, “mwina ana anga achimwa ndipo anyoza+ Mulungu mumtima mwawo.”+ Umu ndi mmene Yobu anali kuchitira nthawi zonse.+  Tsopano linafika tsiku limene ana a Mulungu woona+ ankapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo ngakhalenso Satana+ anapita nawo limodzi.+  Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anamuyankha Yehova kuti: “Ndinali kuzungulirazungulira m’dziko lapansi+ ndi kuyendayendamo.”+  Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu, poti palibe wina wokhala ngati iyeyo padziko lapansi?+ Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa+ ndi wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndi wopewa zoipa.”+  Pamenepo Satana anamuyankha Yehova kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe?+ 10  Kodi inuyo simwam’tchinga iyeyo?+ Mwatchingiranso nyumba yake ndi chilichonse chimene ali nacho. Mwadalitsa ntchito ya manja ake+ ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri padziko lapansi. 11  Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”+ 12  Choncho Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, chilichonse chimene ali nacho chikhale m’manja mwako. Koma iyeyo usam’tambasulire dzanja lako ndi kum’khudza.” Pamenepo Satana anachoka pamaso pa Yehova.+ 13  Tsopano linafika tsiku limene ana a Yobu, aamuna ndi aakazi, anali kudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya m’bale* wawo woyamba kubadwa.+ 14  Kenako kunabwera munthu+ kwa Yobu kudzanena uthenga wakuti: “Ng’ombe zinali kulima+ ndipo abulu aakazi anali kudya msipu chapambali pake. 15  Ndiyeno kunabwera Asabeya+ omwe alanda ziwetozo n’kupha abusa ake ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”+ 16  Uyu ali mkati molankhula kunabwera munthu wina kudzanena kuti: “Moto wa Mulungu watsika kuchokera kumwamba,+ ndipo wayaka pakati pa nkhosa ndi abusa n’kupsereza nkhosazo ndi abusawo. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.” 17  Ameneyu ali mkati molankhula kunabwera munthu wina kudzanena kuti: “Kunabwera magulu atatu a Akasidi+ omwe anafika mwaliwiro kwambiri, n’kulanda ngamila ndi kupha abusa ake ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.” 18  Ameneyu ali mkati molankhula kunabwera munthu winanso kudzanena kuti: “Ana anu aamuna ndi aakazi anali kudya ndi kumwa vinyo+ m’nyumba ya m’bale wawo woyamba kubadwa. 19  Kenako kunabwera chimphepo+ kuchokera kudera la kuchipululu chomwe chinawomba makona anayi a nyumbayo, ndipo nyumbayo yagwera anawo n’kuwapha. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.” 20  Yobu atamva zimenezi anaimirira n’kung’amba+ malaya ake akunja odula manja. Anametanso tsitsi+ kumutu kwake, kenako anagwada pansi+ n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ 21  n’kuyamba kunena kuti:“Ndinatuluka m’mimba mwa mayi anga ndili wamaliseche,+Ndipo ndidzabwerera mmenemo ndilinso wamaliseche.+Yehova wapereka,+ ndipo Yehova yemweyo watenga.+Dzina la Yehova lipitirize kutamandidwa.”+ 22  M’zonsezi Yobu sanachimwe, kapena kunena kuti Mulungu wachita zosayenera.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “mchimwene.”