Yakobo 4:1-17

4  Kodi nkhondo zimene zikuchitika pakati panu zikuchokera kuti? Nanga kukangana pakati panu kukuchokera kuti? Kodi sizikuchokera m’zilakolako za thupi lanu+ zimene zikuchita nkhondo m’ziwalo zanu?+  Mumalakalaka, koma simukhala nazo. Mumapha anthu+ ndiponso mumasirira mwansanje,+ koma simupeza kanthu. Mumakangana+ ndiponso mumachita nkhondo. Simukhala ndi kanthu chifukwa simupempha.  Mumapempha koma simulandira, chifukwa mukupempha ndi cholinga choipa,+ kuti mukhutiritse zilakolako za matupi anu.+  Achigololo+ inu, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu?+ Choncho, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi+ la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.+  Kapena mukuyesa kuti lemba limanena pachabe kuti: “Mzimu umene uli mwa ife uli ndi chizolowezi cholakalaka zinthu zosiyanasiyana”?+  Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+  Choncho gonjerani+ Mulungu, koma tsutsani Mdyerekezi+ ndipo adzakuthawani.+  Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.+ Yeretsani manja anu ochimwa inu,+ ndipo yeretsani mitima yanu,+ okayikakayika inu.+  Imvani chisoni ndipo lirani.+ Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chisangalalo chanu chisanduke chisoni.+ 10  Dzichepetseni pamaso pa Yehova,+ ndipo iye adzakukwezani.+ 11  Abale, muleke kunenerana zoipa.+ Wonenera m’bale wake zoipa kapena woweruza+ m’bale wake, akunenera zoipa lamulo ndi kuweruza lamulo. Choncho ngati ukuweruza lamulo, sukuchita zimene lamulo limanena ayi. Ukukhala woweruza.+ 12  Komatu wopereka lamulo ndi woweruza alipo mmodzi yekha,+ amenenso akhoza kupulumutsa ndi kuwononga.+ Ndiye iwe ndiwe ndani, kuti uziweruza mnzako?+ 13  Tamverani tsopano inu amene mumati: “Lero kapena mawa tipita kumzinda wakutiwakuti ndipo tikatha chaka kumeneko. Tikachita malonda kumeneko ndi kupeza phindu.”+ 14  Mumatero chonsecho simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.+ Pakuti ndinu nkhungu yongoonekera kanthawi kenako n’kuzimiririka.+ 15  M’malomwake, muyenera kunena kuti: “Yehova akalola,+ tikhala ndi moyo, ndi kuchita zakutizakuti.”+ 16  Koma tsopano mumakonda kudzitama.+ Kunyada konse koteroko ndi koipa. 17  Chotero, ngati munthu akudziwa kuchita chabwino koma sakuchichita,+ akuchimwa.+

Mawu a M'munsi