Yakobo 3:1-18

3  Abale anga, pasakhale aphunzitsi ambiri pakati panu,+ podziwa kuti tidzalandira chiweruzo chachikulu.+  Paja tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.+ Ngati wina sapunthwa pa mawu,+ ameneyo ndi munthu wangwiro,+ ndipo akhoza kulamuliranso thupi lake lonse.  Tikamangirira zingwe+ pakamwa pa mahatchi* kuti atimvere,+ timatha kulamuliranso matupi awo onse.  N’chimodzimodzinso ngalawa. Ngakhale kuti ndi zazikulu kwambiri ndipo zimayenda mokankhidwa ndi mphepo zamphamvu, munthu woziyendetsa amaziwongolera ndi thabwa laling’ono+ kuti zipite kumene iye akufuna.  N’chimodzimodzinso lilime. Lilime ndi kachiwalo kakang’ono, koma limadzitama kwambiri.+ Tangoganizani mmene kamoto kakang’onong’ono kamayatsira nkhalango yaikulu.  Lilimenso ndi moto.+ Mwa ziwalo zathu zonse, lilime ndilo lili lodzaza ndi zosalungama chifukwa limadetsa thupi lonse.+ Lili ndi moto wa Gehena* ndipo limayatsa moyo wonse wa munthu.  Pakuti anthu akhala akuweta mtundu uliwonse wa nyama zakutchire, mbalame, ndi zokwawa ndiponso zamoyo zam’nyanja.+  Koma lilime, palibe munthu ndi mmodzi yemwe angathe kuliweta. Ndilo kanthu kamodzi kosalamulirika ndi kovulaza, kodzaza ndi poizoni wakupha.+  Pakuti lilime timatamanda nalo Yehova,+ amenenso ndi Atate,+ komanso ndi lilime lomwelo timatemberera+ anthu amene analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu.”+ 10  Pakamwa pamodzimodzipo pamatuluka mawu otamanda ndi otemberera. N’kosayenera abale anga kuti zinthu zimenezi zipitirire kuchitika motere.+ 11  Kasupe+ satulutsa madzi abwino ndi owawa padzenje limodzi, amatero ngati? 12  Abale anga, kodi mkuyu ungabale maolivi, kapena mtengo wa mpesa ungabale nkhuyu?+ Ngakhale madzi amchere sangatulutse madzi abwino. 13  Kodi pakati panu pali aliyense wanzeru ndi womvetsa zinthu? Ameneyo ayenera kukhala ndi khalidwe labwino limene limasonyeza kuti amachita chilichonse+ mofatsa ndipo kufatsa kwake kumachokera mu nzeru. 14  Koma ngati m’mitima mwanu muli nsanje yaikulu+ ndi kukonda mikangano,+ musadzitamande+ pakuti kutero n’kunamizira choonadi.+ 15  Imeneyo si nzeru yochokera kumwamba,+ koma ya padziko lapansi,+ yauchinyama ndiponso yauchiwanda.+ 16  Pakuti pamene pali nsanje+ ndi mtima wokonda mikangano, palinso chisokonezo ndi zoipa zamtundu uliwonse.+ 17  Koma nzeru+ yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera,+ kenako yamtendere,+ yololera,+ yokonzeka kumvera, yodzaza ndi chifundo ndi zipatso zabwino,+ yopanda tsankho,+ ndiponso yopanda chinyengo.+ 18  Komanso, chilungamo+ ndicho chipatso+ cha mbewu zimene anthu odzetsa mtendere+ amafesa mu mtendere.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Onani Zakumapeto 6.