Yakobo 2:1-26

2  Abale anga, kodi mukuganiza kuti mukukhulupirira Ambuye wathu Yesu Khristu, amene ali ulemerero+ wathu, pamene mukuchita zokondera?+  Pakuti munthu wovala mphete zagolide ndi zovala zapamwamba akafika pamsonkhano+ wanu, ndipo winanso wosauka wovala zovala zonyansa akafika,+  inu mumasangalala ndi wovala zapamwamba uja+ ndipo mumamuuza kuti: “Khalani pamalo pabwinopa,” koma kwa wosauka uja mumati: “Imirira choncho,” kapena: “Khala pansipa pafupi ndi chopondapo mapazi anga.”  Mumasankhana pakati panu+ ndipo mwakhala oweruza+ opereka zigamulo zoipa,+ si choncho kodi?  Tamverani abale anga okondedwa. Mulungu anasankha anthu amene ali osauka+ m’dzikoli kuti akhale olemera+ m’chikhulupiriro ndi olandira cholowa cha ufumu umene anaulonjeza kwa omukonda,+ sanatero kodi?  Koma inu simulemekeza munthu wosauka. Kodi si olemera amene amakusautsani+ ndi kukukokerani kumabwalo amilandu?+  Kodi si iwo amene amanyoza+ dzina labwino kwambiri limene mukuimira?+  Tsopano ngati inu mukutsatira lamulo lachifumu+ lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha,”+ monga mmene lemba limanenera, mukuchita bwino ndithu.  Koma mukapitiriza kukhala okondera,+ mukuchita tchimo, chifukwa lamulo likukutsutsani+ monga ochimwa. 10  Aliyense wosunga Chilamulo akalakwitsa mbali imodzi, walakwira malamulo onse.+ 11  Pakuti amene anati: “Usachite chigololo,”+ anatinso: “Usaphe munthu.”+ Tsopano ngati iwe sunachite chigololo koma wapha munthu, walakwira chilamulo. 12  Muzilankhula ndi kuchita zinthu monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la mfulu.+ 13  Pakuti wosachita chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo.+ Chifundo n’chopambana kwambiri kuposa chiweruzo. 14  Abale anga, kodi pali phindu lanji ngati wina amati ali ndi chikhulupiriro+ koma sachita ntchito zake?+ Kodi chikhulupiriro chimenecho chingamupulumutse?+ 15  Ngati m’bale kapena mlongo ali waumphawi ndipo alibe chakudya chokwanira pa tsikulo,+ 16  koma wina mwa inu n’kunena kuti: “Yendani bwino, mupeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse,” koma osamupatsa zimene thupi lake likusowazo, kodi pali phindu lanji?+ 17  Momwemonso chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake,+ ndi chakufa. 18  Koma wina anganene kuti: “Iweyo uli ndi chikhulupiriro, koma ine ndili ndi ntchito zake. Undionetse chikhulupiriro chako popanda ntchito zake, ndipo ine ndikuonetsa chikhulupiriro changa mwa ntchito.”+ 19  Umakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi, si choncho?+ Ukuchita bwino. Koma ziwanda nazonso zimakhulupirira ndipo zimanjenjemera.+ 20  Mbuli iwe, kodi sukudziwa kuti chikhulupiriro chopanda ntchito zake n’chopanda pake? 21  Kodi Abulahamu atate wathu+ sanayesedwe wolungama chifukwa cha ntchito zake, atapereka Isaki mwana wake nsembe paguwa?+ 22  Waonatu kuti chikhulupiriro chake chinayendera limodzi ndi ntchito zake, ndipo mwa ntchito zakezo chikhulupiriro chakecho chinakhala changwiro.+ 23  Choncho linakwaniritsidwa lemba limene limati, “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova,* ndipo anaonedwa ngati wolungama,”+ choncho anatchedwa “bwenzi la Yehova.”+ 24  Mukuonatu kuti munthu amaonedwa ngati wolungama+ chifukwa cha ntchito zake,+ osati chifukwa cha chikhulupiriro chokha.+ 25  N’chimodzimodzinso ndi Rahabi.+ Kodi Rahabi hule lija, silinaonedwe ngati lolungama chifukwa cha ntchito zake, powalandira bwino azondi aja ndi kuwabweza kwawo powasonyeza njira ina?+ 26  Ndithudi, monga mmene thupi lopanda mzimu limakhalira lakufa,+ nachonso chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.