Yakobo 1:1-27
1 Ine Yakobo,+ kapolo+ wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, ndikupereka moni kwa mafuko 12+ amene ali obalalika:+
2 Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana,+
3 monga mukudziwira kuti chikhulupiriro chanu chikayesedwa, chimabala kupirira.+
4 Koma mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira+ ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kalikonse.+
5 Choncho ngati wina akusowa nzeru,+ azipempha kwa Mulungu,+ ndipo adzamupatsa,+ popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.+
6 Koma azipempha+ ndi chikhulupiriro, osakayikira m’pang’ono pomwe,+ pakuti wokayikira ali ngati funde lapanyanja lotengeka ndi mphepo+ ndi lowindukawinduka.
7 Munthu wotero asaganize kuti adzalandira kanthu kwa Yehova,+
8 chifukwa choti iye ndi wokayikakayika,+ wosakhazikika+ m’njira zake zonse.
9 Koma m’bale wonyozeka akondwere chifukwa tsopano wakwezedwa,+
10 ndipo wachuma+ akondwere chifukwa tsopano watsitsidwa, chifukwa mofanana ndi duwa la zomera, wachumayo adzafota.+
11 Dzuwa limatuluka ndi kutentha kwake n’kufotetsa zomera, ndipo maluwa a zomerazo amathothoka. Kukongola kwake kumatha. Momwemonso munthu wachuma adzafa akutsatira njira ya moyo wake.+
12 Wodala ndi munthu wopirira mayesero,+ chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira mphoto* ya moyo,+ umene Yehova analonjeza onse omukonda.+
13 Munthu akakhala pa mayesero+ asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.
14 Koma munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake.+
15 Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.+ Nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.+
16 Abale anga okondedwa, musasocheretsedwe.+
17 Mphatso iliyonse yabwino+ ndi yangwiro imachokera kumwamba,+ pakuti imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zonse zakuthambo,+ ndipo iye sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.+
18 Pakuti mwa chifuniro+ chake, iye anatibala ife ndi mawu a choonadi.+ Anachita zimenezi kuti tikhale zipatso zoyambirira+ pa zolengedwa zake.
19 Abale anga okondedwa, dziwani izi: Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula,+ wosafulumira kukwiya,+
20 chifukwa mkwiyo wa munthu subala chilungamo cha Mulungu.+
21 Choncho siyani khalidwe lililonse lonyansa ndiponso siyani khalidwe lochita zoipa, lomwe ndi losafunika,+ ndipo vomerezani mofatsa mawu okhoza kupulumutsa miyoyo yanu,+ kuti abzalidwe mwa inu.+
22 Komabe muzichita zimene mawu amanena,+ osati kungomva chabe, n’kumadzinyenga ndi maganizo onama.+
23 Pakuti ngati munthu ali wongomva mawu, koma wosachita,+ ali ngati munthu wodziyang’anira nkhope yake pagalasi.
24 Iye amadziyang’ana koma akachokapo, nthawi yomweyo amaiwala kuti ndi munthu wotani.
25 Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro+ limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala+ polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.+
26 Ngati munthu akudziona ngati wopembedza,+ koma salamulira lilime lake,+ ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake,+ kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.+
27 Kupembedza koyera+ ndi kosaipitsidwa+ kwa Mulungu ndi Atate wathu ndi uku: Kusamalira ana amasiye+ ndi akazi amasiye+ m’masautso awo,+ ndi kukhala wopanda banga+ la dzikoli.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”