Tito 2:1-15

2  Koma iwe pitiriza kulankhula zinthu zogwirizana ndi chiphunzitso cholondola.+  Amuna achikulire+ akhale osachita zinthu mopitirira malire, opanda chibwana,+ oganiza bwino, achikhulupiriro cholimba,+ achikondi chachikulu, ndi opirira+ kwambiri.  Chimodzimodzinso akazi achikulire.+ Akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza. Asakhale amiseche,+ kapena akapolo a vinyo wambiri, koma akhale aphunzitsi a zinthu zabwino,  kuti azikumbutsa akazi achitsikana kukonda amuna+ awo, kukonda ana+ awo,  kukhala oganiza bwino, oyera,+ ogwira ntchito zapakhomo, abwino ndi ogonjera+ amuna awo, kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.+  Mofanana ndi zimenezi, pitiriza kulimbikitsa anyamata kuti akhale oganiza bwino.+  M’zinthu zonse, ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino.+ Chiphunzitso+ chako chikhale chopanda chinyengo.+ Usonyeze kuti ndiwe wopanda chibwana.  Mawu ako akhale oyenera amene sangatsutsike,+ kuti munthu wotsutsa achite manyazi, ndipo asapeze choipa chotinenera nacho.+  Akapolo+ azigonjera ambuye awo pa zonse+ ndipo aziwakondweretsa. Asamatsutsane nawo+ 10  kapena kuwabera,+ koma akhale okhulupirika pa chilichonse,+ kuti akometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi+ wathu Mulungu, m’zinthu zonse. 11  Pakuti Mulungu waonetsa+ kukoma mtima kwake kwakukulu+ kumene kumabweretsa chipulumutso+ kwa anthu, kaya akhale a mtundu wotani.+ 12  Zimenezi zatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu+ ndi zilakolako za dziko,+ koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu+ m’nthawi* ino.+ 13  Tizichita zimenezi pamene tikuyembekeza kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo+ chosangalatsa ndi kuonetsedwa kwaulemerero+ kwa Mulungu wamkuluyo ndiponso kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu. 14  Iyeyo anadzipereka+ m’malo mwa ife kuti atilanditse+ ku moyo wochita zinthu zosamvera malamulo za mtundu uliwonse ndiponso kuti atiyeretse,+ kuti tikhale anthu akeake,+ odzipereka pa ntchito zabwino.+ 15  Pitiriza kulankhula zimenezi, kulimbikitsa ndi kudzudzula anthu mogwirizana ndi ulamuliro wonse umene wapatsidwa.+ Munthu aliyense asakuderere.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.