Rute 4:1-22

4  Zitatero, Boazi anapita kuchipata.+ Kumeneko iye anakhala pansi. Ali chikhalire choncho, anaona wowombola anam’tchula uja+ akudutsa. Ndiyeno Boazi anati: “Iwe Uje takhotera pano, khala pansi apa.” Motero anakhota n’kukhala pansi.  Kenako anatenga amuna 10 mwa akulu+ a mzindawo n’kuwauza kuti: “Khalani pansi.” Iwo anakhaladi pansi.  Ndiyeno Boazi anauza wowombola+ uja kuti: “Naomi amene wabwerera kuchokera kudziko la Mowabu+ ayenera kugulitsa munda umene unali wa m’bale wathu Elimeleki.+  Ndiye ine ndaganiza zoti ndikuuze kuti, ‘Ugule mundawo+ pamaso pa anthu ndi pamaso pa akulu a mzinda uno.+ Ngati ukufuna kuuwombola, uwombole. Koma ngati sukufuna undiuze kuti ndidziwe, popeza palibenso wina amene angauwombole koma iweyo,+ pambuyo pako pali ine.’” Pamenepo, wowombola uja anati: “Ndiuwombola ineyo.”+  Kenako Boazi anati: “Ukadzagula mundawo kwa Naomi, ndiye kuti waugulanso kwa Rute Mmowabu, amene mwamuna wake anamwalira, kuti dzina la mwamuna wakeyo libwerere pacholowa chake.”+  Poyankha wowombolayo anati: “Sinditha kuuwombola, kuopera kuti ndingawononge cholowa changa. Iweyo uuwombole m’malo mwa ine, chifukwa ine sinditha kuuwombola.”  Tsopano, kale mu Isiraeli munali mwambo wokhudza ufulu wowombola ndiponso wokhudza kusinthana ufuluwo, pofuna kuti atsimikizirane chilichonse. Mwambo wake unali wotere: Munthu anali kuvula nsapato+ yake ndi kuipereka kwa mnzake. Uwu ndiwo unali umboni wotsimikizirana mu Isiraeli.  Choncho pamene wowombola uja anauza Boazi kuti: “Ugule iweyo,” wowombolayo anavula nsapato yake.+  Kenako Boazi anauza akulu ndi anthu onse kuti: “Inu ndinu mboni+ lero kuti ndikugula kwa Naomi zonse zimene zinali za Elimeleki, ndi zonse zimene zinali za Kiliyoni ndi Maloni. 10  Komanso ndikugula Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni, kukhala mkazi wanga kuti dzina la mwamuna wake amene anamwalira+ libwerere pacholowa chake, kutinso lisafafanizike pakati pa abale ake ndi mumzinda wathu. Inu ndinu mboni+ lero.” 11  Pamenepo anthu onse ndi akulu amene anali pachipata anayankha kuti: “Ndife mboni! Yehova adalitse mkazi amene akulowa m’nyumba mwako kuti akhale ngati Rakele+ ndi Leya,+ akazi amene anabereka ana a nyumba ya Isiraeli.+ Uonetse kulemekezeka kwako mu Efurata+ ndi kudzipangira dzina m’Betelehemu.+ 12  Ndipo kudzera mwa ana amene Yehova adzakupatsa kwa mtsikanayu,+ nyumba yako ikhale ngati nyumba ya Perezi, amene Tamara anaberekera Yuda.”+ 13  Choncho Boazi anatenga Rute kukhala mkazi wake ndipo anagona naye. Pamenepo Yehova anam’dalitsa ndipo anatenga pakati+ n’kubereka mwana wamwamuna. 14  Zitatero akazi anayamba kuuza+ Naomi kuti: “Adalitsike Yehova,+ amene wachititsa kuti usasowe wokuwombola lero, kuti dzina lake lifalitsidwe mu Isiraeli. 15  Mwanayu watsitsimutsa moyo wako ndipo adzakusamalira mu ukalamba wako,+ chifukwa wabadwa kwa mpongozi wako amene amakukonda,+ amenenso ndi woposa ana aamuna 7.”+ 16  Choncho Naomi ananyamula mwanayo, ndipo anakhala mlezi wake. 17  Pamenepo akazi okhala naye pafupi+ anatcha mwanayo dzina lakuti Obedi.+ Ndipo iwo anati: “Mwana wabadwa kwa Naomi.” Obedi ndiye bambo ake a Jese,+ bambo ake a Davide. 18  Tsopano uwu ndiwo mzere wa mbadwa za Perezi:+ Perezi anabereka Hezironi,+ 19  Hezironi anabereka Ramu, Ramu+ anabereka Aminadabu, 20  Aminadabu+ anabereka Naasoni,+ Naasoni anabereka Salimoni, 21  Salimoni+ anabereka Boazi, Boazi+ anabereka Obedi, 22  Obedi anabereka Jese,+ ndipo Jese anabereka Davide.+

Mawu a M'munsi