Rute 3:1-18

3  Tsopano Naomi, apongozi a Rute, anamuuza kuti: “Mwana wanga, kodi sindiyenera kukupezera mpumulo,+ kuti zikuyendere bwino?  Wakhala ukukunkha pambuyo pa atsikana antchito a Boazi. Kodi iye si wachibale wathu?+ Pajatu usiku walero akhala akupeta+ balere pamalo ake opunthira.  Choncho samba ndi kudzola mafuta+ ndi kuvala zovala+ ndipo upite kopunthirako. Koma iye asakuzindikire mpaka atamaliza kudya ndi kumwa.  Ndiyeno pamene akugona, ukaone kuti wagona pati. Ukapite pamene wagonapo ndi kuvundukula kumapazi ake ndi kugona pomwepo. Ndipo iye adzakuuza zoti uchite.”  Pamenepo Rute anamuyankha Naomi kuti: “Zonse zimene mwanena ndikachita.”  Ndipo anapita kopunthirako n’kuchita zonse zimene apongozi ake anamuuza.  Boazi anadya ndi kumwa, ndipo anali wosangalala mumtima mwake.+ Kenako anapita kukagona chakumapeto kwa mulu wa balere. Ndiyeno Rute anayenda mwakachetechete ndi kuvundukula kumapazi kwa Boazi n’kugona.  Ndiye pakati pa usiku Boazi anayamba kunjenjemera. Chotero anadzuka n’kukhala tsonga. Koma anadabwa kuona mkazi atagona kumapazi ake!  Pamenepo anafunsa kuti: “Ndiwe yani?” Poyankha, Rute anati: “Ndine Rute kapolo wanu. Mufunditse kapolo wanu chovala chanu, pakuti ndinu wotiwombola.”+ 10  Atatero, Boazi anati: “Yehova akudalitse,+ mwana wanga. Kukoma mtima kosatha+ kumene wasonyeza panopa kukuposa koyamba kuja,+ popeza sunafune anyamata, kaya osauka kapena olemera. 11  Tsopano usachite mantha mwana wanga. Ndidzakuchitira zonse zimene wanena,+ chifukwa aliyense mumzinda wathu akudziwa kuti ndiwe mkazi wabwino kwambiri.+ 12  Komano ngakhale kuti ndinedi wokuwombolani,+ pali wachibale wina wapafupi kwambiri kuposa ine+ amene angakuwombole. 13  Gona pompano lero. Ngati iye angakuwombole+ mawa, zili bwino! Akuwombole. Koma ngati sakufuna kukuwombola, ineyo ndidzakuwombola. Ndithudi, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ ndidzakuwombola. Gona kufikira m’mawa.” 14  Choncho anagonabe kumapazi a Boazi kufikira m’mawa, kenako anadzuka kudakali mdima. Boazi sanafune kuti anthu adziwe kuti kopunthira mbewuko kunafika mkazi.+ 15  Ndiyeno anamuuza kuti: “Bwera nayo kuno nsalu wafundayo, uitambasule.” Iye anaitambasula, ndipo Boazi anathirapo miyezo 6* ya balere ndi kum’senza pamutu. Zitatero, Boazi analowa mumzinda. 16  Tsopano Rute anabwerera kwa apongozi ake, ndipo anam’funsa kuti: “Ndiwe yani, mwana wanga?” Pamenepo anawafotokozera zonse zimene Boazi anam’chitira. 17  Anafotokozanso kuti: “Wandipatsa balere uyu, wokwana miyezo 6, n’kundiuza kuti, ‘Usapite kwa apongozi ako chimanjamanja.’”+ 18  Atatero, Naomi anayankha kuti: “Dekha, mwana wanga, kufikira utadziwa mmene nkhaniyi ithere. Chifukwa iye sakhala pansi mpaka ataithetsa nkhaniyi lero.”+

Mawu a M'munsi

Malinga ndi mabuku a Arabi, imeneyi inali miyezo 6 ya seya kapena kuti malita 44. Zikuoneka kuti zimenezi ndizo akanakwanitsa kusenza pamutu.