Rute 2:1-23

2  Panali munthu wina wolemera kwambiri+ yemwe anali wachibale+ wa mwamuna wake wa Naomi. Dzina lake anali Boazi,+ wa kubanja la Elimeleki.  Tsiku lina Rute mkazi wachimowabu uja anapempha Naomi kuti: “Chonde ndiloleni ndipite kuminda ndikakunkhe+ balere m’mbuyo mwa aliyense amene angandikomere mtima.” Ndipo Naomi anamuyankha kuti: “Pita mwana wanga.”  Pamenepo Rute ananyamuka n’kupita, ndipo anakalowa m’munda wina ndi kuyamba kukunkha m’mbuyo mwa okolola.+ Mwamwayi mundawo unali wa Boazi,+ wa ku banja la Elimeleki.+  Kenako Boazi anafika kuchokera ku Betelehemu ndipo anauza okololawo kuti: “Yehova akhale nanu.”+ Iwo anayankha mwa nthawi zonse kuti: “Yehova akudalitseni.”+  Pamenepo Boazi+ anafunsa mnyamata amene anamuika kukhala kapitawo kuti: “Nanga kodi mtsikana uyu ndi wochokera ku banja liti?”  Kapitawoyo anayankha kuti: “Mtsikana ameneyu ndi Mmowabu+ amene anabwera limodzi ndi Naomi kuchokera ku Mowabu.+  Iyeyu atafika anapempha kuti, ‘Chonde ndikunkheko.+ Ndizitola balere wotsala m’mbuyo mwa okololawo.’ Atatero, analowa m’mundamu n’kuyamba kukunkha. Wakhala akukunkha kuyambira m’mawa mpaka posachedwapa pamene anakhala pansi pang’ono m’chisimbamu.”*+  Kenako Boazi anauza Rute kuti: “Tamvera mwana wanga, usapitenso kumunda wina kukakunkha.+ Usachoke pano kupita kwina, ukhale pafupi ndi atsikana anga antchitowa.+  Maso ako akhale pamunda umene akukolola, ndipo uzipita nawo limodzi kumeneko. Anyamatawa ndawalamula kuti asakukhudze.+ Ukamva ludzu, nawenso uzipita kumitsuko kukamwa madzi amene anyamatawa azitunga.”+ 10  Atamva zimenezo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ n’kunena kuti: “Zatheka bwanji kuti mundiganizire ndi kundikomera mtima chotere, ine wokhala mlendo?”+ 11  Ndiyeno Boazi anamuyankha kuti: “Ndamva zonse zimene wachitira apongozi ako chimwalilireni mwamuna wako.+ Ndamvanso kuti unasiya bambo ako ndi mayi ako, komanso dziko la abale ako, n’kubwera kuno kwa anthu amene sunali kuwadziwa n’kale lonse.+ 12  Yehova akudalitse chifukwa cha zimene wachita,+ ndipo Yehova, Mulungu wa Isiraeli akufupe mokwanira.+ Iye amene m’mapiko mwake wathawiramo ndi kupezamo chitetezo.”+ 13  Atamva zimenezi Rute anati: “Mwandikomera mtima mbuyanga. Mwanditonthoza mtima, komanso mwalankhula mondilimbitsa mtima+ ngati kuti ndine mtsikana wanu wantchito pamene sindili mmodzi wa atsikana anu antchito.”+ 14  Ndipo pa nthawi ya chakudya Boazi anaitana Rute kuti: “Tabwera kuno udzadye mkate+ ndiponso uziusunsa mu vinyo wowawasayu.” Choncho Rute anadzakhala pansi limodzi ndi okololawo, ndipo Boazi anali kum’patsira mbewu zokazinga,+ iye n’kumadya moti anakhuta mpaka zina kutsala. 15  Atatha kudya ananyamuka kukayambanso kukunkha.+ Tsopano Boazi analamula anyamata ake kuti: “Muloleni akunkhe pomwe mwadula kale balere, ndipo musam’vutitse.+ 16  Komanso, muzisololapo balere wina pamitolopo n’kumamusiya pansi kuti iye akunkhe.+ Ndipo musamuletse.” 17  Choncho Rute anapitiriza kukunkha m’mundamo kufikira madzulo.+ Atamaliza anapuntha+ balere amene anakunkhayo moti anakwana pafupifupi muyezo umodzi wa efa.*+ 18  Kenako ananyamula balereyo ndi kubwerera kumzinda, ndipo apongozi ake anaona balere amene anakunkhayo. Pambuyo pake, Rute anatenga chakudya chimene chinatsalako+ atakhuta chija n’kupatsa apongozi ake. 19  Tsopano apongozi ake anam’funsa kuti: “Kodi unakakunkha kuti lero? Adalitsike amene wakuganizirayo.”+ Ndiyeno iye anauza apongozi akewo za mwinimunda umene anakakunkhamo, kuti: “Dzina la mwinimunda umene ndakunkhamo lero ndi Boazi.” 20  Pamenepo Naomi anauza mpongozi wakeyo kuti: “Yehova amene sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha+ kwa amoyo ndi akufa,+ am’dalitse munthu ameneyu.”+ Ndipo Naomi anapitiriza kuti: “Munthuyutu ndi wachibale wathu.+ Ndi mmodzi wa otiwombola.”+ 21  Ndiyeno Rute mkazi wachimowabuyo anati: “Moti anandiuzanso kuti, ‘Usachoke, uzikhala pafupi ndi antchito angawa mpaka adzamalize kundikololera zonse.’”+ 22  Ndipo Naomi+ anauza Rute mpongozi wake+ kuti: “Ndi bwinodi mwana wanga, uzipita limodzi ndi atsikana akewo, kuopera kuti angakakunyoze ukapita kumunda wina.”+ 23  Choncho Rute anapitiriza kukhala pafupi ndi atsikana antchito a Boazi, mpaka pamene anamaliza kukolola balere+ ndi tirigu. Ndipo anapitiriza kukhala ndi apongozi ake.+

Mawu a M'munsi

Kanyumba ka kumunda. Mawu ena, “khumbi” kapena “dindiro.”
“Muyezo umodzi wa efa” ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.