Rute 1:1-22

1  Tsopano zinachitika kuti, m’masiku amene oweruza+ anali atsogoleri, m’dzikomo munagwa njala.+ Ndiyeno munthu wina anasamuka ku Betelehemu+ wa ku Yuda kukakhala m’dziko la Mowabu+ monga mlendo. Anasamuka ndi mkazi wake ndi ana ake awiri aamuna.  Munthuyo dzina lake anali Elimeleki, ndipo mkazi wake anali Naomi. Mayina a ana akewo anali Maloni ndi Kiliyoni. Anthuwa anali a ku Betelehemu Efurata+ wa ku Yuda. Ndipo anafika m’dziko la Mowabu ndi kukhazikika kumeneko.  Patapita nthawi, Elimeleki mwamuna wa Naomi anamwalira, moti Naomi anatsala ndi ana ake awiriwo.  Kenako, anawo anakwatira akazi achimowabu.+ Wina dzina lake anali Olipa, wina anali Rute.+ Ndipo anakhalabe kumeneko zaka pafupifupi 10.  Patapita nthawi, ana awiriwo, Maloni ndi Kiliyoni, nawonso anamwalira, moti Naomi anatsala yekha wopanda ana ake awiri aja, komanso wopanda mwamuna.  Pamenepo iye limodzi ndi apongozi ake anakonzekera ulendo wochoka kudziko la Mowabu, chifukwa ali kumeneko anamva kuti Yehova wakumbukira anthu ake+ powapatsa chakudya.+  Chotero Naomi pamodzi ndi apongozi ake awiri aja ananyamuka kumene anali kukhalako,+ n’kuyamba ulendo wobwerera kudziko la Yuda.  Kenako Naomi anauza apongozi akewo kuti: “Basi bwererani, aliyense apite kunyumba kwa amayi ake. Yehova akusonyezeni kukoma mtima kosatha+ ngati mmenenso inuyo munasonyezera kukoma mtima kumeneko kwa amuna anu amene anamwalira ndiponso kwa ine.+  Yehova akudalitseni.+ Aliyense apeze mpumulo+ m’nyumba ya mwamuna wake.” Kenako anawapsompsona.+ Pamenepo iwo anayamba kulira mokweza mawu, 10  ndipo anaumirira kuti: “Ayi musatero, ife tipita nanu kwanu.”+ 11  Koma Naomi anati: “Bwererani ana anga. Palibe chifukwa choti tipitire limodzi. Kodi ndingathenso kubereka ana, ndipo kodi anawo angadzakhale amuna anu?+ 12  Bwererani ana anga, pitani, popeza ndakalamba kwambiri moti sindingakwatiwenso. Ngakhale n’tanena kuti ndikwatiwa pofika usiku wa lero n’kubereka ana aamuna,+ 13  kodi mungawadikirirebe mpaka atakula? Kodi mungadzisungebe osakwatiwa powadikirira? Ayi ndithu ana anga, zimene zinakuchitikirani zimandiwawa kwambiri, pakuti dzanja la Yehova landiukira.”+ 14  Atatero iwo analiranso mokweza mawu. Kenako Olipa anapsompsona apongozi ake powatsanzika. Koma Rute anawaumirirabe.+ 15  Choncho Naomi anati: “Taona m’bale wako wamasiye wabwerera kwa anthu a kwawo ndi kwa milungu yake.+ Bwerera naye limodzi.”+ 16  Ndiyeno Rute anati: “Musandichonderere kuti ndikusiyeni, kuti ndibwerere ndisakutsatireni, pakuti kumene inu mupite inenso ndipita komweko, kumene inu mugone inenso ndigona komweko.+ Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga,+ ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.+ 17  Kumene inu mudzafere inenso ndidzafera komweko,+ ndipo ndidzaikidwanso komweko. Yehova andilange kwambiri+ ngati chinachake kupatulapo imfa chingandilekanitse ndi inu.” 18  Ataona kuti walimbikira zoti apite naye limodzi,+ anasiya kumuuza kuti abwerere. 19  Ndipo anapitiriza ulendo wawo mpaka anafika ku Betelehemu.+ Atangofika ku Betelehemu, anthu mumzinda wonsewo anayamba kulankhula za iwo.+ Akazi anali kufunsa kuti: “Kodi si Naomi+ uyu?” 20  Koma iye powayankha anali kunena kuti: “Musanditchulenso kuti Naomi,* muzinditchula kuti Mara,* chifukwa Wamphamvuyonse+ wachititsa moyo wanga kukhala wowawa kwambiri.+ 21  Ndinali ndi zonse pochoka kuno,+ koma Yehova wandibweza wopanda kanthu.+ Munditchuliranji kuti Naomi, pamene ndi Yehova amene wandichititsa kukhala wonyozeka,+ ndipo ndi Wamphamvuyonseyo amene wandigwetsera tsokali?”+ 22  Umu ndi mmene Naomi anabwererera kwawo. Anabwerera ndi Rute mkazi wachimowabu, mpongozi wake, kuchokera kudziko la Mowabu.+ Iwo anafika ku Betelehemu+ kumayambiriro kwa nyengo yokolola balere.+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Mara” limatanthauza “Kuwawa.”
Dzina lakuti “Naomi” limatanthauza “Kusangalatsa Kwanga.”