Nyimbo ya Solomo 8:1-14

8  “Ndikulakalaka ukanakhala ngati mlongo wanga,+ amene anayamwa mabere a mayi anga.+ Ndikanakupeza panja ndikanakupsompsona,+ ndipo anthu sakanandinyoza n’komwe.  Bwenzi nditakutsogolera ndipo ndikanakulowetsa m’nyumba mwa mayi anga,+ amene ankandiphunzitsa. Ndikanakupatsa vinyo wothira zonunkhiritsa,+ ndi madzi a makangaza ongofinya kumene.  Dzanja lake lamanzere likanakhala pansi pa mutu wanga, ndipo dzanja lake lamanja likanandikumbatira.+  “Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu, kuti musayese kudzutsa chikondi mwa ine mpaka pamene chikondicho chifunire.”+  “Kodi mkazi+ amene akuchokera kuchipululuyu ndani,+ atakoloweka dzanja lake m’khosi mwa wachikondi wake?”+ “Ine ndinakudzutsa pansi pa mtengo wa maapozi. Pamenepo m’pamene mayi ako anamva zowawa pokubereka. Mayi amene anali kukubereka anamva zowawa ali pamenepo.+  “Undiike pamtima pako ngati chidindo,+ ndiponso undiike ngati chidindo padzanja lako, chifukwa chikondi n’champhamvu ngati imfa.+ Mofanana ndi Manda,* chikondi sichigonja ndipo chimafuna kudzipereka ndi mtima wonse.+ Kuyaka kwake kuli ngati kuyaka kwa moto. Chikondicho ndi lawi la Ya.*+  Madzi ambiri sangathe kuzimitsa chikondi,+ ndipo mitsinje singachikokolole.+ Munthu atapereka zinthu zonse zamtengo wapatali za m’nyumba mwake posinthanitsa ndi chikondi, anthu anganyoze zinthuzo.”  “Tili ndi mlongo wathu wamng’ono+ amene alibe mabere. Kodi tidzamuchitire chiyani tsiku limene adzafunsiridwe ukwati?”  “Akadzakhala khoma,+ tidzam’mangira kansanja kasiliva pamwamba pake, koma akadzakhala chitseko,+ tidzam’khomerera ndi thabwa la mkungudza.” 10  “Ine ndine khoma, ndipo mabere anga ali ngati nsanja.+ Choncho m’maso mwake ndakhala ngati mkazi amene wapeza mtendere. 11  “Solomo anali ndi munda wa mpesa+ ku Baala-hamoni. Munda wa mpesawo anaupereka kwa anthu oti aziusamalira.+ Munthu aliyense anali kubweretsa ndalama zasiliva zokwana 1,000 zolipirira zipatso za mundawo. 12  “Munda wanga wa mpesa ndingathe kuchita nawo chilichonse. Ndalama 1,000 zasilivazo ndi zanu inu a Solomo, ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za anthu amene amatenga zipatso za munda wanu wa mpesa.” 13  “Iwe amene ukukhala m’minda,+ anzanga* akufuna amve mawu ako. Inenso ndikufuna ndimve mawu ako.”+ 14  “Thamanga wachikondi wanga. Ukhale ngati insa kapena ngati mphoyo yaing’ono pamapiri pamene pamamera maluwa onunkhira.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 5.
Awa ndi malo okhawo m’buku la Nyimbo ya Solomo pamene pakupezeka dzina la Mulungu. Panopa, lalembedwa mwachidule kuti “Ya.” Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2 ndi Zakumapeto 1.
Mwina akutanthauzanso, “anzako.”