Nyimbo ya Solomo 5:1-16

5  “Ndabwera m’munda mwanga,+ iwe mlongo wanga,+ mkwatibwi wanga.+ Ndathyola mule+ wanga limodzi ndi zonunkhiritsa zanga. Ndadya chisa changa cha uchi limodzi ndi uchi wanga.+ Ndamwa vinyo wanga limodzi ndi mkaka wanga.” “Idyani, inu anthu okondana! Imwani ndipo muledzere ndi chikondi chimene mukusonyezana.”+  “Panopa ndili m’tulo koma mtima wanga uli maso.+ Ndikumva wachikondi wanga akugogoda.”+ “Nditsegulire+ iwe mlongo wanga, wokondedwa wanga, njiwa yanga, iwe wopanda chilema.+ Pakuti m’mutu mwanga mwadzaza mame, ndipo tsitsi langa ladzaza madontho a madzi a usiku.”+  “‘Ndavula mkanjo wanga. Kodi ndiuvalenso? Ndatsuka mapazi anga. Kodi ndiwadetsenso?’  Wachikondi wanga atachotsa dzanja lake pabowo la chitseko, m’mimba mwanga+ munabwadamuka.  Ine ndinadzuka kuti ndimutsegulire wachikondi wanga ndipo manja anga anali kuyenderera mafuta a mule. Zala zanga zinali kuyenderera mule pamene ndinali kugwira pabowo lolowetsapo loko wa pachitseko.  Ndinam’tsegulira wachikondi wanga, koma wachikondi wangayo anali atachokapo, atapita. Moyo wanga unachoka mwa ine nditamva mawu ake. Ndinam’funafuna koma sindinam’peze.+ Ndinamuitana koma sanandiyankhe.  Alonda+ amene anali kuyendayenda mumzinda anandipeza. Anandimenya, anandivulaza. Alonda a pamipanda+ anandilanda chofunda changa.  “Ndakulumbiritsani+ inu ana aakazi a ku Yerusalemu+ kuti mukam’peza wachikondi wanga,+ mumuuze kuti ine chikondi chikundidwalitsa.”+  “Kodi wachikondi wako akuposa bwanji achikondi ena onse,+ iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse?+ Kodi wachikondi wako akuposa bwanji achikondi ena onse, kuti utilumbiritse lumbiro lotereli?”+ 10  “Wachikondi wanga ndi wokongola ndipo khungu lake ndi lofiirira. Pa amuna 10,000, iye ndiye wooneka bwino kwambiri.+ 11  Mutu wake ndi wokongola ngati golide, golide woyengedwa bwino. Tsitsi lake lili ngati zipatso za kanjedza. Tsitsi lakelo ndi lakuda ngati khwangwala. 12  Maso ake ali ngati njiwa zimene zili pafupi ndi mtsinje wamadzi, zimene zikusamba mumkaka, zitakhala chakumphepete kwa madziwo. 13  Masaya ake ali ngati bedi la m’munda la maluwa onunkhira,+ ndiponso ngati nsanja zomangidwa ndi zitsamba zonunkhira. Milomo yake ili ngati maluwa amene akuchucha mafuta a mule.+ 14  Zala zake zonenepa bwino ndi zagolide, ndipo zikhadabo zake ndi zakulusolito. Mimba yake ndi yopangidwa ndi minyanga ya njovu yokutidwa ndi miyala ya safiro. 15  Miyendo yake ili ngati zipilala zamiyala ya mabo zozikidwa pazitsulo zokhala ndi mphako, zagolide woyengedwa bwino. Iye ndi wokongola ngati dziko la Lebanoni ndipo palibe wofanana naye pa nkhani ya kukongola, mofanana ndi mitengo ya mkungudza.+ 16  M’kamwa mwake ndi mokoma kwambiri ndipo chilichonse mwa iye n’chosiririka.+ Ameneyu ndiye wachikondi wanga ndipo ameneyutu ndiye wokondedwa wanga, inu ana aakazi a ku Yerusalemu.”

Mawu a M'munsi