Nyimbo ya Solomo 4:1-16

4  “Ndiwe wokongola kwabasi,+ wokondedwa wanga. Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa+ munsalu yako yophimba kumutuyo.+ Tsitsi lako likuoneka ngati gulu la mbuzi+ zimene zikudumphadumpha potsetsereka kuchokera kudera lamapiri la Giliyadi.+  Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zazikazi zomwe angozimeta kumene,+ zimene zikuchokera kozisambitsa, zonse zitabereka mapasa, popanda imene ana ake afa.  Milomo yako ili ngati chingwe chofiira kwambiri, ndipo kulankhula kwako n’kosangalatsa.+ M’mbali mwa mutu wako muli ngati khangaza* logamphula pakati, munsalu yako yophimba kumutuyo.+  Khosi lako+ lili ngati nsanja+ ya Davide. Lili ngati nsanja yomangidwa ndi miyala yokhala m’mizeremizere, yomwe akolekapo zishango 1,000, zishango zonse zozungulira+ za amuna amphamvu.  Mabere ako awiri+ ali ngati ana awiri aang’ono, ngati ana amapasa a insa yaikazi, amene akudya msipu pakati pa maluwa akutchire.”+  “Nthawi ya kamphepo kayaziyazi isanakwane+ ndiponso mithunzi isanachoke, ndipita kuphiri la mule ndiponso kuphiri la lubani.”+  “Ndiwe wokongola paliponse,+ wokondedwa wanga, ndipo mwa iwe mulibe chilema chilichonse.+  Tiye tichokere limodzi ku Lebanoni, iwe mkwatibwi wanga,+ tiye tichoke ku Lebanoni.+ Utsetsereke kuchokera pamwamba pa phiri la Amana, kuchokera pamwamba pa phiri la Seniri,+ ngakhalenso pamwamba pa phiri la Herimoni.+ Utsetsereke kuchokera m’mapanga a mikango, ndiponso kuchokera kumapiri a akambuku.*  Wachititsa mtima wanga kugunda, iwe mlongo wanga,+ mkwatibwi wanga.+ Wachititsa mtima wanga kugunda ndi diso lako limodzi lokha,+ ndiponso ndi diso limodzi lokha la mkanda wa m’khosi mwako. 10  Chikondi chimene umandisonyeza n’chokoma,+ iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga. Chikondi chimene umandisonyeza n’chabwino kuposa vinyo ndipo kununkhira kwa mafuta ako odzola n’koposa zonunkhira za mitundu yonse.+ 11  Milomo yako imangokhalira kukha uchi wapachisa,+ iwe mkwatibwi wanga. Uchi+ ndi mkaka zili kuseri kwa lilime lako, ndipo kununkhira kwa zovala zako kuli ngati kununkhira+ kwa nkhalango ya Lebanoni. 12  Mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ali ngati munda wotchingidwa ndi mpanda.+ Iye ali ngati munda wotchingidwa ndi mpanda, ndiponso ngati kasupe wotsekedwa. 13  Khungu lako lili ngati munda wokongola* wokhala ndi mitengo ya makangaza ya zipatso zabwino kwambiri,+ mitengo ya maluwa ofiirira, mitengo ya nado,+ 14  maluwa a safironi,+ mabango onunkhira,+ sinamoni,+ komanso mitengo yosiyanasiyana ya lubani, mule, aloye,+ ndi zonunkhira zonse zabwino kwambiri.+ 15  Khungu lako lilinso ngati kasupe wa m’munda, chitsime cha madzi abwino,+ ndiponso timitsinje tochokera ku Lebanoni.+ 16  Dzuka, iwe mphepo yakumpoto. Bwera, iwe mphepo yakum’mwera.+ Womba pamunda wanga+ kuti kununkhira kwake kumveke.” “Wachikondi wanga alowe m’munda wake kuti adzadye zipatso zake zokoma kwambiri.”

Mawu a M'munsi

“Khangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.
Ena amati “anyalugwe.”
Mawu ake enieni, “paradaiso.”