Nyimbo ya Solomo 3:1-11

3  “Pabedi panga usiku, ndinaganizira za munthu amene mtima wanga umam’konda.+ Ndinalakalaka kumuona koma iye panalibe.  Chotero ndinati: ‘Ndidzuke ndikazungulire mumzinda,+ m’misewu ndi m’mabwalo a mumzinda,+ kuti ndikafunefune munthu amene mtima wanga umam’konda.’ Ndinam’funafuna koma sindinamupeze.  Alonda+ amene anali kuzungulira mumzindawo anandipeza, ndipo ine ndinawafunsa kuti: ‘Kodi amuna inu, mwamuonako munthu amene mtima wanga umam’konda?’  Nditangowapitirira pang’ono, ndinam’peza munthu amene mtima wanga umam’konda. Ndinamugwira ndipo sindinafune kum’siya mpaka nditamubweretsa m’nyumba mwa mayi anga, m’chipinda chamkati cha mayi amene anali ndi pakati kuti ine ndibadwe.  Ndakulumbiritsani inu+ ana aakazi a ku Yerusalemu, pali mbawala zazikazi ndiponso pali mphoyo zakutchire,+ kuti musayese kudzutsa chikondi mwa ine mpaka pamene chikondicho chifunire.”+  “Kodi chinthu chikuchokera kuchipululuchi n’chiyani, chooneka ngati utsi wokwera m’mwamba, chonunkhira mafuta a mule, lubani,*+ ndi mtundu uliwonse wa zonunkhira za ufa za munthu wamalonda?”+  “Taonani! Ndi bedi la Solomo. Amuna 60 amphamvu ochokera mwa amuna amphamvu a Isiraeli alizungulira.+  Onsewo atenga malupanga ndipo ndi ophunzitsidwa nkhondo. Aliyense wamangirira lupanga lake m’chiuno mwake kuti adziteteze ku zoopsa za usiku.”+  “Ndi bedi* limene Mfumu Solomo inadzipangira ndi mitengo ya ku Lebanoni.+ 10  Mizati yake ndi yasiliva. Motsamira mwake ndi mwagolide. Pokhalira pake ndi popangidwa ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira. Mkati mwake, ana aakazi a ku Yerusalemu akongoletsamo posonyeza chikondi.” 11  “Inu ana aakazi a Ziyoni, pitani panja mukaone Mfumu Solomo itavala nkhata yamaluwa,+ imene mayi ake+ anailukira pa tsiku la ukwati wake, pa tsiku limene mtima wa mfumuyo unasangalala.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Limeneli linali bedi lochita kunyamula, limene anali kunyamulirapo munthu wolemekezeka.