Nyimbo ya Solomo 2:1-17

2  “Ine ndine duwa lonyozeka+ la m’chigwa cha m’mphepete mwa nyanja.+ Inetu ndine duwa la m’chigwa.”+  “Monga duwa pakati pa zitsamba zaminga, ndi mmene alili wokondedwa wanga pakati pa ana aakazi.”+  “Monga mtengo wa maapozi+ pakati pa mitengo ya m’nkhalango, ndi mmene alili wachikondi wanga pakati pa ana aamuna.+ Ineyo ndinali kulakalaka mthunzi wa wokondedwa wanga ndipo ndinakhala pansi, pamthunzi wakewo. Chipatso chake chinali chotsekemera* m’kamwa mwanga.  Iye anandipititsa kunyumba ya phwando la vinyo,+ ndipo chikondi+ chake kwa ine chinali ngati mbendera+ yozikidwa pambali panga.  Anthu inu ndipatseni mphesa zouma zoumba pamodzi kuti zinditsitsimule.+ Ndipatseni maapozi kuti ndisafe chifukwa chikondi chikundidwalitsa.+  Dzanja lake lamanzere lili pansi pa mutu wanga, ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.+  Ndakulumbiritsani inu+ ana aakazi a ku Yerusalemu, pali mbawala zazikazi+ ndiponso pali mphoyo+ zakutchire, kuti musayese kudzutsa chikondi mwa ine mpaka pamene chikondicho chifunire.+  “Ndikumva wachikondi wanga+ akubwera.+ Akukwera mapiri ndipo akudumphadumpha pazitunda.  Wachikondi wanga akufanana ndi mbawala+ kapena mphoyo yaing’ono. Taonani! Iye waima kuseri kwa khoma* la nyumba yathu. Akuyang’ana m’mawindo,* akusuzumira pa zotchingira m’mawindo.+ 10  Wachikondi wanga wandiuza kuti, ‘Nyamuka wokondedwa wanga wokongolawe,+ tiye tizipita.+ 11  Taona! Nyengo yamvula yatha,+ mvula yaleka, yapita kwawo. 12  Maluwa ayamba kuoneka m’dziko,+ nthawi yodulira mpesa+ yakwana, ndipo m’dziko lathu mukumveka kulira kwa njiwa.+ 13  Pamtengo wa mkuyu,+ nkhuyu zoyambirira zapsa.+ Mpesa wachita maluwa ndipo ukununkhira. Nyamuka, bwera kuno wokondedwa wanga+ wokongola, tiye tizipita. 14  Iwe njiwa yanga,+ tuluka m’malo obisika a pathanthwe. Tuluka pamalo osaoneka m’mphepete mwa njira yotsetsereka. Ndikufuna ndione thupi lako lokongola.+ Ndikufuna kumva mawu ako, chifukwa mawu ako ndi okoma ndipo iweyo ndiwe wokongola.’”+ 15  “Anthu inu mutigwirire nkhandwe+ zing’onozing’ono zimene zikuwononga minda ya mpesa, chifukwa minda yathu ya mpesa yachita maluwa.”+ 16  “Wachikondi wanga ndi wanga, ndipo ine ndine wake.+ Iye akudyetsera ziweto msipu+ umene uli pakati pa maluwa am’tchire.+ 17  Mpaka nthawi ya kamphepo kayaziyazi ndiponso mpaka mithunzi itachoka, tembenuka wachikondi wanga. Ukhale ngati mbawala+ kapena ngati mphoyo yaing’ono pamapiri amene akutilekanitsa.

Mawu a M'munsi

Ena amati “chonzuna.”
Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”
Pawindo limeneli panali potchingidwa ndi timatabwa tolukanalukana.