Nehemiya 9:1-38

9  Pa tsiku la 24 la mwezi umenewu+ ana a Isiraeli anasonkhana pamodzi. Iwo anali kusala kudya+ atavala ziguduli*+ ndiponso atadzithira dothi+ kumutu.  Pamenepo mbewu ya Isiraeli inadzipatula+ kwa anthu onse osakhala Aisiraeli.+ Atatero anaimirira ndi kuulula+ machimo awo+ ndi zolakwa za makolo awo.+  Iwo anaimirira pomwepo+ ndipo anawerenga mokweza buku la chilamulo+ cha Yehova Mulungu wawo kwa maola atatu.*+ Kwa maola enanso atatu anali kuulula machimo awo+ ndi kugwadira Yehova Mulungu wawo.+  Ndiyeno Yesuwa, Bani, Kadimiyeli, Sebaniya,+ Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani anakwera pansanja+ ya Alevi ndi kuyamba kufuula kwa Yehova Mulungu wawo ndi mawu amphamvu.+  Choncho Yesuwa, Kadimiyeli, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya, omwe anali Alevi, anati: “Dzukani, tamandani+ Yehova Mulungu wanu kuyambira kalekale mpaka kalekale.*+ Inu Mulungu wathu, anthuwa atamande dzina lanu laulemerero,+ lokwezeka kuposa dalitso ndi chitamando chilichonse.  “Inu ndinu Yehova, inu nokha.+ Ndinu amene munapanga kumwamba,+ ngakhale kumwambamwamba ndi makamu ake onse.+ Ndinu amene munapanga dziko lapansi+ ndi zonse zili momwemo+ komanso nyanja+ ndi zonse zili momwemo.+ Ndinu amene mukusunga zinthu zonse kuti zikhale ndi moyo. Ndipo makamu+ akumwamba amakugwadirani.  Inu ndinu Yehova Mulungu woona, amene munasankha Abulamu+ ndi kum’tulutsa ku Uri wa Akasidi+ ndipo munamutcha dzina lakuti Abulahamu.+  Munamuona kuti anali ndi mtima wokhulupirika pamaso panu.+ Chotero munachita naye pangano+ kuti mudzam’patsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Munachita naye pangano kuti mudzapereka dziko limeneli kwa mbewu yake,+ ndipo munachitadi zimene munanena chifukwa ndinu wolungama.+  “Choncho inu munaona+ nsautso ya makolo athu ku Iguputo ndipo munamvanso kulira kwawo pa Nyanja Yofiira.+ 10  Ndiyeno munaonetsa Farao zizindikiro ndi zozizwitsa zomukhaulitsa pamodzi ndi atumiki ake onse ndi anthu onse okhala m’dziko lake.+ Munatero chifukwa munadziwa kuti iwo anachita zinthu modzikuza+ kwa makolo athu. Pamenepo munadzipangira dzina+ kufikira lero. 11  Munagawa nyanja+ pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja.+ Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama+ ngati mwala+ woponyedwa m’madzi amphamvu.+ 12  Usana munali kuwatsogolera ndi mtambo woima njo ngati chipilala,+ ndipo usiku munali kuwatsogolera ndi moto woima njo ngati chipilala+ kuti uziwaunikira+ njira imene anayenera kuyendamo. 13  Ndiyeno munatsikira paphiri la Sinai+ ndi kulankhula nawo muli kumwamba.+ Munawapatsa zigamulo zowongoka+ ndi malamulo a choonadi,+ mfundo zabwino ndi malangizo abwino.+ 14  Munawaphunzitsa za sabata lanu lopatulika.+ Munawapatsa malangizo, mfundo ndi chilamulo kudzera mwa Mose mtumiki wanu.+ 15  Munawapatsanso mkate wochokera kumwamba kuti athetse njala yawo.+ Munatulutsa madzi pathanthwe ndi kuwapatsa kuti athetse ludzu lawo,+ ndiyeno munawauza kuti alowe+ ndi kutenga dziko limene munalumbira mutakweza dzanja lanu kuti mudzawapatsa.+ 16  “Koma iwo, makolo athu, anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi lawo+ ndipo sanamvere malamulo anu. 17  Choncho iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire+ zochita zanu zodabwitsa zimene munawachitira, m’malomwake anaumitsa khosi lawo+ ndipo anasankha mtsogoleri+ kuti awatsogolere pobwerera ku ukapolo wawo ku Iguputo. Koma inu ndinu Mulungu wokhululuka,+ wachisomo+ ndi wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha,+ chotero simunawasiye.+ 18  Pamene anasungunula chitsulo n’kudzipangira chifanizo cha mwana wa ng’ombe+ n’kuyamba kunena kuti, ‘Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani mu Iguputo,’+ ndipo anachita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani, 19  inuyo simunawasiye m’chipululu chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ Mtambo woima njo ngati chipilala sunawachokere usana ndipo unali kuwatsogolera,+ ngakhalenso moto woima njo ngati chipilala sunawachokere usiku ndipo unali kuwaunikira njira imene anayenera kuyendamo.+ 20  Munawapatsa mzimu wanu wabwino+ kuti akhale anzeru. Simunawamane mana+ ndipo munawapatsa madzi kuti athetse ludzu lawo.+ 21  Kwa zaka 40+ munawapatsa chakudya m’chipululu. Iwo sanasowe kanthu.+ Zovala zawo sizinathe+ ndipo mapazi awo sanatupe.+ 22  “Pamenepo munawapatsa maufumu+ ndi mitundu ya anthu ndipo munawagawira dzikolo chigawo ndi chigawo.+ Iwo anatenga dziko la Sihoni,+ dziko la mfumu ya Hesiboni+ ndi dziko la Ogi+ mfumu ya Basana.+ 23  Ndipo munawachulukitsira ana awo ngati nyenyezi zakumwamba.+ Mutatero munawalowetsa m’dziko+ limene munalonjeza makolo awo+ kuti akalowe ndi kulitenga. 24  Choncho ana awo+ analowa ndi kutenga dzikolo,+ ndipo munagonjetsa+ anthu okhala m’dzikolo, Akanani,+ ndi kuwapereka m’manja mwawo. Munaperekanso ngakhale mafumu a Akananiwo+ ndi mitundu ya anthu ya m’dzikolo+ kwa ana a Isiraeliwo kuti awachite zimene akufuna.+ 25  Iwo analanda mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Analandanso nthaka yachonde,+ nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino,+ zitsime,*+ minda ya mpesa ndi ya maolivi+ ndi mitengo ya zipatso yochuluka. Atatero, anayamba kudya, kukhuta,+ kunenepa+ ndi kukondwera ndi ubwino wanu waukulu.+ 26  “Koma iwo anakhala osamvera+ ndipo anakupandukirani.+ Anapitiriza kufulatira chilamulo chanu,+ ndipo anapha aneneri anu+ amene anali kuwalimbikitsa kuti abwerere kwa inu.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani.+ 27  Chifukwa chochita zimenezi, munawapereka m’manja mwa adani awo+ amene anapitiriza kuwasautsa.+ Koma akakumana ndi nsautso, anali kukulirirani,+ ndipo inu munali kumva muli kumwambako.+ Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu,+ munali kuwapatsa owapulumutsa+ amene anali kuwalanditsa m’manja mwa adani awo.+ 28  “Koma akangokhala pa mtendere, anali kuchitanso zoipa pamaso panu+ ndipo munali kuwasiya m’manja mwa adani awo amene anali kuwapondaponda.+ Zikatero, anali kubweranso kwa inu ndi kupempha thandizo lanu,+ ndipo inu munali kumva muli kumwambako+ ndi kuwapulumutsa mobwerezabwereza, chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ 29  Ngakhale kuti munali kuwalimbikitsa+ kuti abwerere ku chilamulo chanu,+ iwo anali kuchita zinthu modzikuza+ ndipo sanali kumva malamulo anu. Anachimwira zigamulo zanu,+ zimene ngati munthu azitsatira adzakhala ndi moyo chifukwa cha zigamulozo.+ Iwo anatseka makutu*+ awo ndi kuumitsa khosi+ lawo ndipo sanamvere.+ 30  Koma munaleza nawo mtima kwa zaka zambiri+ ndipo munapitirizabe kuwachenjeza+ mwa mzimu wanu potumiza aneneri anu, koma iwo sanamvere.+ Pamapeto pake munawapereka m’manja mwa mitundu ya anthu ya m’dzikolo.+ 31  Koma mwachifundo chanu chachikulu simunawafafanize+ kapena kuwasiya,+ pakuti inu ndinu Mulungu wachisomo+ ndi wachifundo.+ 32  “Tsopano Mulungu wathu, Mulungu wamkulu,+ wamphamvu+ ndi wochititsa mantha,+ wosunga pangano+ ndi kusonyeza kukoma mtima kosatha,+ musachepetse+ mavuto onse amene agwera ifeyo,+ mafumu athu,+ akalonga athu,+ ansembe athu,+ aneneri athu,+ makolo athu+ ndi anthu anu onse kuchokera masiku a mafumu a Asuri mpaka lero.+ 33  Inu ndinu wolungama+ pa zinthu zonse zimene zatichitikira, pakuti inu mwachita zinthu mokhulupirika+ koma ife tachita zinthu zoipa.+ 34  Mafumu athu, akalonga athu, ansembe athu ndi makolo athu+ sanatsatire chilamulo chanu+ ndipo sanamvere malamulo anu+ kapena zikumbutso zanu zowachenjeza.+ 35  Iwo sanakutumikireni+ ndipo sanabwerere kusiya zoipa zimene anali kuchita+ pamene anali ndi mafumu+ komanso pamene munali kuwapatsa zabwino zochuluka,+ m’dziko lalikulu ndi lachonde+ limene munawapatsa. 36  Onani, lero ife ndife akapolo.+ Ndife akapolo m’dziko limene munapatsa makolo athu kuti adye zipatso zake ndi zinthu zake zabwino.+ 37  Zokolola za m’dzikoli zachulukira+ mafumu+ amene mwatiikira chifukwa cha machimo athu.+ Iwo akulamulira matupi athu komanso ziweto zathu mmene akufunira, ndipo tili pamavuto aakulu.+ 38  “Choncho chifukwa cha zimenezi, tikuchita pangano lodalirika+ ndi kulilemba, ndipo akalonga athu, Alevi athu ndi ansembe athu akutsimikizira panganoli ndi chidindo chawo.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”
Mawu ake enieni, “gawo lachinayi la tsiku.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “phewa laliuma.”