Nehemiya 8:1-18

8  Ndiyeno anthu onse anasonkhana pamodzi mogwirizana+ m’bwalo lalikulu+ limene linali pafupi ndi Chipata cha Kumadzi.+ Pamenepo anthuwo anauza Ezara+ wokopera Malemba kuti abweretse buku+ la chilamulo cha Mose+ limene Yehova analamula Aisiraeli kuti azilitsatira.+  Choncho Ezara wansembe+ anabweretsa chilamulo pamaso pa mpingo+ wa amuna komanso akazi ndi ana onse amene akanatha kumvetsera ndi kuzindikira+ zimene zinali kunenedwa. Limeneli linali tsiku loyamba la mwezi wa 7.+  Ezara anawerenga+ mokweza bukulo m’bwalo lalikulu limene linali pafupi ndi Chipata cha Kumadzi, kuyambira m’mawa+ mpaka masana. Anali kuwerenga bukuli pamaso pa amuna, akazi ndi ana amene akanatha kumvetsera ndi kuzindikira. Anthu onse anatchera khutu kuti amve+ zimene zinali m’buku la chilamuloli.  Ezara wokopera Malembayo, anaimirira pansanja yamatabwa+ imene inamangidwa chifukwa cha mwambo umenewu. Pafupi naye, kudzanja lake lamanja kunaimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya, ndi Maaseya. Ndipo kudzanja lake lamanzere kunaimirira Pedaya, Misayeli, Malikiya,+ Hasumu,+ Hasi-badana, Zekariya ndi Mesulamu.  Ndiyeno Ezara anatsegula+ bukulo pamaso pa anthu onse, pakuti iye anaimirira pamalo okwera kusiyana ndi anthu onse. Pamene iye anali kutsegula bukulo anthu onse anaimirira.+  Kenako Ezara anatamanda Yehova+ Mulungu woona, Mulungu wamkulu. Atatero anthu onse anakweza manja awo m’mwamba+ ndi kuyankha kuti, “Ame! Ame!”*+ Ndiyeno anthuwo anagwada+ ndi kuwerama pamaso pa Yehova mpaka nkhope zawo pansi.+  Pamenepo Alevi anali kufotokozera anthu chilamulocho,+ anthuwo ataimirira.+ Alevi amenewo anali Yesuwa, Bani, Serebiya,+ Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseya, Kelita, Azariya, Yozabadi,+ Hanani ndi Pelaya.+  Iwo anapitiriza kuwerenga+ bukulo mokweza. Anapitiriza kuwerenga chilamulo cha Mulungu woona, kuchifotokozera ndi kumveketsa tanthauzo lake. Iwo anapitiriza kuthandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuwerenga.+  Ndiyeno Nehemiya+ amene ndiye Tirisata+ komanso Ezara+ wansembe, wokopera Malemba, ndi Alevi amene anali kupereka malangizo kwa anthu, anauza anthuwo kuti: “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu.+ Musakhale achisoni ndipo musalire.”+ Ananena zimenezi chifukwa anthu onse anali kulira pamene anali kumvetsera mawu a m’chilamulo.+ 10  Nehemiya anapitiriza kunena kuti: “Pitani mukadye zinthu zonona, kumwa zinthu zokoma ndi kugawa chakudya+ kwa anthu amene sanathe kudzikonzera chakudya, pakuti lero ndi tsiku lopatulika kwa Ambuye wathu. Choncho musadzimvere chisoni pakuti chimwemwe chimene Yehova amapereka ndicho malo anu achitetezo.” 11  Ndiyeno Alevi anali kuuza anthu onse kuti akhale chete ndipo anati: “Khalani chete! pakuti lero ndi tsiku lopatulika, musadzimvere chisoni.” 12  Choncho anthu onse anapita kukadya, kukamwa, kukagawira ena chakudya+ ndi kukondwera kwambiri+ chifukwa anamvetsa bwino mawu amene anawafotokozera.+ 13  Tsiku lachiwiri, atsogoleri a mabanja a anthu onse komanso ansembe ndi Alevi, anasonkhana pamodzi pamaso pa Ezara wokopera Malemba, kuti amvetse bwino mawu a m’chilamulo.+ 14  Pamenepo anapeza kuti m’chilamulo chimene Yehova anawapatsa kudzera mwa Mose+ analembamo kuti ana a Isiraeli azikhala m’misasa+ pa nthawi ya chikondwerero m’mwezi wa 7.+ 15  Analembamonso kuti azilengeza+ ndi kufuula m’mizinda yonse ndi mu Yerusalemu monse+ kuti: “Pitani kumapiri+ mukatenge nthambi za mitengo ya maolivi,+ nthambi za mitengo ya mafuta, nthambi za mitengo ya mchisu, masamba akanjedza ndi nthambi za mitengo ya masamba ambiri kuti mudzapangire misasa mogwirizana ndi zolembedwa.” 16  Pamenepo anthu anatuluka ndi kukatenga zinthu zimenezi ndipo anapangira misasa. Aliyense anapanga msasa pamwamba pa nyumba yake+ komanso m’mabwalo awo, m’mabwalo+ a nyumba ya Mulungu woona, m’bwalo lalikulu+ la Chipata cha Kumadzi+ ndiponso m’bwalo lalikulu la Chipata cha Efuraimu.+ 17  Choncho mpingo wonse wa anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo anamanga misasa ndi kukhala m’misasayo. Panali chisangalalo chachikulu kwambiri+ chifukwa chakuti ana a Isiraeli anali asanachitepo zimenezi kuchokera m’masiku a Yoswa mwana wa Nuni,+ mpaka kudzafika tsiku limeneli. 18  Ndiyeno tsiku ndi tsiku, kuchokera tsiku loyamba mpaka tsiku lomaliza, anali kuwerenga mokweza buku la chilamulo cha Mulungu woona.+ Iwo anachita chikondwererocho masiku 7, ndipo pa tsiku la 8 anachita msonkhano wapadera malinga ndi lamulo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”