Nehemiya 7:1-73

7  Ndiyeno mpanda utangotha kumangidwanso,+ ndinaika zitseko zake.+ Kenako ndinaika alonda a m’zipata,+ oimba+ ndi Alevi.+  Zitatero ndinaika Haneni+ m’bale wanga ndi Hananiya kalonga wa m’Nyumba ya Chitetezo Champhamvu,+ kuti aziyang’anira Yerusalemu. Hananiya anali munthu wodalirika+ ndipo anali woopa kwambiri+ Mulungu woona kuposa anthu ena ambiri.  Choncho ndinawauza kuti: “Zipata+ za Yerusalemu siziyenera kutsegulidwa kufikira dzuwa litatentha. Alonda a m’zipatazo atseke zitseko ndi kuzikhoma ndi akapichi ndipo aime pafupi.+ Muikenso alonda a anthu okhala mu Yerusalemu, ena muwaike pamalo awo olondera ndipo ena muwaike kutsogolo kwa nyumba zawo.”+  Tsopano mzindawo unali wotakasuka ndi waukulu. Mkati mwake munali anthu ochepa+ ndipo sanamangemo nyumba.  Koma Mulungu wanga anaika nzeru mumtima mwanga+ kuti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu onse kuti alembetse mayina awo motsatira mzere wawo wobadwira.+ Ndiyeno ndinapeza buku la mndandanda wa mayina a mzere wobadwira+ wa anthu amene anabwera moyambirira kuchokera ku ukapolo. Ndinapeza kuti m’bukumo analembamo izi:  Awa ndi anthu a m’chigawo+ amene anatuluka mu ukapolo+ wa anthu omwe Nebukadinezara+ mfumu ya ku Babulo anawatengera ku ukapolo ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+  Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,+ Nehemiya, Azariya,* Raamiya,* Nahamani, Moredekai,+ Bilisani, Misiperete,* Bigivai, Nehumu,* ndi Bana. Chiwerengero cha amuna a Isiraeli ndi ichi:  Ana a Parosi,+ 2,172.  Ana a Sefatiya,+ 372. 10  Ana a Ara,+ 652. 11  Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu,+ 2,818. 12  Ana a Elamu,+ 1,254. 13  Ana a Zatu,+ 845. 14  Ana a Zakai,+ 760. 15  Ana a Binui,+ 648. 16  Ana a Bebai,+ 628. 17  Ana a Azigadi,+ 2,322. 18  Ana a Adonikamu,+ 667. 19  Ana a Bigivai,+ 2,067. 20  Ana a Adini,+ 655. 21  Ana a Ateri,+ a m’nyumba ya Hezekiya, 98. 22  Ana a Hasumu,+ 328. 23  Ana a Bezai,+ 324. 24  Ana a Harifi,+ 112. 25  Ana a Gibeoni,+ 95. 26  Amuna a ku Betelehemu+ ndi ku Netofa,+ 188. 27  Amuna a ku Anatoti,+ 128. 28  Amuna a ku Beti-azimaveti,+ 42. 29  Amuna a ku Kiriyati-yearimu,+ Kefira,+ ndi ku Beeroti,+ 743. 30  Amuna a ku Rama+ ndi ku Geba,+ 621. 31  Amuna a ku Mikemasi,+ 122. 32  Amuna a ku Beteli+ ndi ku Ai,+ 123. 33  Amuna a ku Nebo wina,+ 52. 34  Ana a Elamu wina,+ 1,254. 35  Ana a Harimu,+ 320. 36  Ana a Yeriko,+ 345. 37  Ana a Lodi,+ Hadidi+ ndi Ono,+ 721. 38  Ana a Senaya,+ 3,930. 39  Ansembe: Ana a Yedaya,+ a m’nyumba ya Yesuwa, 973. 40  Ana a Imeri,+ 1,052. 41  Ana a Pasuri,+ 1,247. 42  Ana a Harimu,+ 1,017. 43  Alevi: Ana a Yesuwa, a m’nyumba ya Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodeva,+ 74. 44  Oimba,+ ana a Asafu,+ 148. 45  Alonda a pachipata,+ ana a Salumu,+ ana a Ateri, ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita, ana a Sobai,+ 138. 46  Anetini:+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,+ 47  ana a Kerosi, ana a Siya,* ana a Padoni,+ 48  ana a Lebana, ana a Hagaba,+ ana a Salimai, 49  ana a Hanani,+ ana a Gideli, ana a Gahara, 50  ana a Reyaya,+ ana a Rezini,+ ana a Nekoda, 51  ana a Gazamu, ana a Uziza, ana a Paseya, 52  ana a Besai,+ ana a Meyuni, ana a Nefusesimu,*+ 53  ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,+ 54  ana a Baziliti,* ana a Mehida, ana a Harisa,+ 55  ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,+ 56  ana a Neziya, ana a Hatifa.+ 57  Ana a atumiki a Solomo:+ Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida,*+ 58  ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,+ 59  ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu, ana a Amoni.*+ 60  Anetini onse+ pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392. 61  Ndiyeno amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri,+ ndipo sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera, kuti kaya anali ochokera mu Isiraeli kapena ayi, ndi awa: 62  ana a Delaya, ana a Tobia, ana a Nekoda,+ 642. 63  Ansembe+ anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi+ ana a Barizilai+ amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ Mgiliyadi ndipo anayamba kutchedwa ndi dzina lawo. 64  Amenewa ndiwo anayang’ana mayina awo m’kaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanawapeze.+ Zitatero anawaletsa kuti asatumikire monga ansembe chifukwa anali oipitsidwa.+ 65  Pa chifukwa chimenechi, Tirisata*+ anawauza kuti sayenera kudya+ zinthu zopatulika koposa kufikira patakhala wansembe wokhala ndi Urimu+ ndi Tumimu.+ 66  Mpingo wonsewo monga gulu limodzi unali ndi anthu 42,360,+ 67  kupatulapo akapolo awo aamuna+ ndi akapolo awo aakazi amene analipo 7,337.+ Iwo analinso ndi oimba aamuna+ ndi aakazi+ 245. 68  Anali ndi mahatchi 736 ndi nyulu* 245.+ 69  Ngamila+ zinalipo 435. Abulu analipo 6,720.+ 70  Ndiye panali atsogoleri+ ena a nyumba za makolo+ amene anapereka mphatso zothandizira pa ntchito.+ Tirisata+ anapereka ndalama za dalakima* zagolide 1,000, mbale zikuluzikulu 50, ndi mikanjo ya ansembe 530 kumalo osungira chuma.+ 71  Ndiyeno panalinso atsogoleri ena a nyumba za makolo amene anapereka mphatso zothandizira pa ntchitoyo kumalo osungira chuma. Iwo anapereka ndalama za dalakima zagolide 20,000, ndi ndalama za mina* zasiliva 2,200.+ 72  Zimene anthu ena onse anapereka zinakwana ndalama za dalakima zagolide 20,000, ndalama za mina zasiliva 2,000 ndi mikanjo ya ansembe 67. 73  Ndiyeno ansembe,+ Alevi, alonda a pazipata, oimba,+ anthu ena onse pamodzi ndi Anetini+ ndi Isiraeli yense anapita kukakhala m’mizinda yawo.+ Pofika mwezi wa 7+ ana a Isiraeli anali atakhala m’mizinda yawo.+

Mawu a M'munsi

Pa Eza 2:2 akutchedwa “Seraya.”
Pa Eza 2:2 akutchedwa “Reelaya.”
Pa Eza 2:2 akutchedwa “Misipara.”
Pa Eza 2:2 akutchedwa “Rehumu.”
Pa Eza 2:44 akutchedwa “Siyaha.”
Pa Eza 2:50 akutchedwa “Nefusimu.”
Pa Eza 2:52 akutchedwa “Baziluti.”
Pa Eza 2:55 akutchedwa “Peruda.”
Pa Eza 2:57 akutchedwa “Ami.”
Onani mawu a m’munsi pa Eza 2:63.
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 2:69.
Onani Zakumapeto 12.