Nehemiya 6:1-19

6  Ndiyeno Sanibalati,+ Tobia,+ Gesemu+ Mluya+ ndi adani athu onse atangouzidwa kuti ndamanganso mpanda,+ ndipo palibe mpata umene watsala (ngakhale kuti kufikira pa nthawiyo ndinali ndisanaike zitseko+ m’zipata zake),+  nthawi yomweyo Sanibalati ndi Gesemu ananditumizira uthenga wakuti: “Tiye tipangane nthawi kuti tikumane+ m’mudzi wina wa m’chigwa cha Ono.”+ Koma anali kundikonzera chiwembu.+  Choncho ndinawatumizira amithenga+ kuti akawauze kuti: “Ntchito imene ndikugwirayi ndi yaikulu,+ sindingathe kupita kumeneko. Kodi ntchitoyi iime chifukwa chakuti ine ndabwera kwa inu?”+  Koma iwo ananditumizira uthenga wofananawo maulendo anayi, ndipo ine ndinali kuwayankha chimodzimodzi.  Kenako Sanibalati+ ananditumizira uthenga wofananawo ulendo wachisanu kudzera mwa mtumiki wake. Mtumikiyo anali ndi kalata yosatseka m’manja mwake.  M’kalatayo analemba kuti: “Zamveka pakati pa anthu a mitundu ina ndipo Gesemu+ akunenanso zomwezo, kuti iwe ndi Ayuda mukufuna kupanduka.+ N’chifukwa chake iwe ukumanga mpandawo, ndipo malinga ndi zimene zikumvekazi, iweyo ukufuna kukhala mfumu yawo.+  Komanso waika aneneri kuti azilengeza za iwe mu Yerusalemu monse kuti, ‘Dziko la Yuda lili ndi mfumu!’ Ife tikanena zinthu zimenezi kwa mfumu. Choncho bwera tikambirane.”+  Koma ine ndinamutumizira uthenga wonena kuti: “Palibe amene wachita zimene ukunenazi,+ koma wangozipeka mumtima mwako.”+  Onsewo anali kungofuna kutichititsa mantha, ndipo anali kunena kuti: “Manja awo+ adzalefuka ndipo adzasiya kugwira ntchitoyi, mwakuti siitha.” Inu Mulungu wanga, limbitsani manja anga.+ 10  Ndiyeno ine ndinalowa m’nyumba ya Semaya mwana wamwamuna wa Delaya, mwana wamwamuna wa Mehetabele, amene anali atadzitsekera m’nyumba.+ Iye anandiuza kuti: “Tipangane nthawi kuti tikakumane+ kunyumba ya Mulungu woona, m’kachisi,+ ndi kutseka zitseko za kachisiyo, pakuti akubwera kudzakupha, ngakhale usiku+ akubwera ndithu kudzakupha.” 11  Koma ine ndinati: “Kodi mwamuna ngati ine ndingathawe?+ Kodi munthu ngati ine angalowe m’kachisi ndi kukhala ndi moyo?+ Ine sindikalowamo!” 12  Nditafufuza ndinapeza kuti sanatumidwe ndi Mulungu,+ koma Tobia ndi Sanibalati+ anamulemba ganyu+ kuti andinenere+ ulosi woipa umenewu. 13  Iwo anamulemba ganyu+ n’cholinga choti ndichite mantha+ kuti ndikalowe m’kachisi ndi kuchimwa.+ Mwakutero, akanandiipitsira dzina langa+ kuti azindinyoza.+ 14  Inu Mulungu wanga, kumbukirani+ zinthu zonse zimene Tobia+ ndi Sanibalati anachita. Mukumbukirenso Nowadiya mneneri wamkazi+ ndi aneneri ena onse amene anali kuyesetsabe kundiopseza. 15  Patapita nthawi, ntchito yomanga mpanda+ inatha pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli.* Ntchitoyi inatenga masiku 52. 16  Ndiyeno adani athu onse atangomva zimenezi,+ komanso anthu a mitundu ina yotizungulira ataona, anachita manyazi ndipo anadziwa kuti ntchito imeneyi yatheka chifukwa cha Mulungu wathu.+ 17  Komanso masiku amenewo, anthu olemekezeka+ a mu Yuda anali kulemberana makalata ambiri ndi Tobia.+ 18  Pakuti anthu ambiri mu Yuda anamulumbirira kukhala naye mwamtendere chifukwa anali mkamwini wa Sekaniya, mwana wamwamuna wa Ara.+ Ndipo Yehohanani mwana wamwamuna wa Tobia, anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu,+ mwana wamwamuna wa Berekiya. 19  Komanso anthu amenewa anali kunena zinthu zabwino za Tobia pamaso panga nthawi zonse.+ Anthuwo anali kutenga zimene ine ndanena ndi kukauza Tobia. Ndipo Tobia anali kundilembera makalata ondiopseza.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 13.