Nehemiya 5:1-19

5  Tsopano amuna ena pamodzi ndi akazi awo anayamba kudandaula kwambiri+ ndipo anali kutsutsana ndi abale awo achiyuda.+  Ena anali kunena kuti: “Tikumapereka ana athu aamuna ndi ana athu aakazi monga chikole kuti tipeze chakudya ndi kukhala ndi moyo.”+  Ndipo ena anali kunena kuti: “Nthawi ya njala, tikumapereka minda yathu ya tirigu, minda yathu ya mpesa ndi nyumba zathu monga chikole+ kuti tipeze chakudya.”  Enanso anali kunena kuti: “Ife takongola ndalama kuti tikhome msonkho kwa mfumu+ wa minda yathu ya tirigu ndi minda yathu ya mpesa.+  Komatu ife ndi anzathuwo ndife pachibale.+ Ana athu aamuna n’chimodzimodzi ndi ana awo aamuna, koma ife tikusandutsa ana athu aamuna ndi ana athu aakazi kukhala akapolo.+ Ndipotu ena mwa ana athu aakazi tawasandutsa kale akapolo. Ife tilibenso mphamvu, chifukwa minda yathu ya tirigu ndi minda yathu ya mpesa ili m’manja mwa anthu ena.”  Pamenepo ine ndinakwiya kwambiri nditangomva kudandaula kwawo komanso mawu amenewa.  Choncho ndinayamba kuganiza mumtima mwanga ndipo ndinapeza kuti anthu olemekezeka ndi atsogoleri anali olakwa.+ Pamenepo ndinawauza kuti: “Nonsenu mukuumiriza abale anu kukupatsani chiwongoladzanja chokwera kwambiri.”+ Kenako ndinaitanitsa msonkhano waukulu chifukwa cha iwowa.+  Ndipo ndinawauza kuti: “Ife tachita zonse zimene tikanatha mwa kuwombola+ abale athu achiyuda amene anagulitsidwa kwa anthu a mitundu ina. Kodi pa nthawi imodzimodziyo inu mukugulitsa abale anu,+ ndipo kodi ife tiwawombole?” Pamenepo anangokhala chete, kusowa chonena.+  Ndiyeno ndinati: “Zimene mukuchitazi si zabwino ayi.+ Kodi simuyenera kuyenda moopa+ Mulungu+ kuti tipewe chitonzo+ cha adani athu, anthu a mitundu ina?+ 10  Ndiponso ine, abale anga ndi atumiki anga, tikukongoza ndalama ndi chakudya kwa abale athu. Chonde, tiyeni tileke kulandira chiwongoladzanja tikakongoza zinthu.+ 11  Chonde, lero abwezereni minda yawo ya tirigu,+ minda yawo ya mpesa, minda yawo ya maolivi, nyumba zawo ndi limodzi mwa magawo 100 a ndalama, tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta zimene munalandira kwa iwo monga chiwongoladzanja.” 12  Pamenepo iwo anati: “Tiwabwezera,+ ndipo sitiwaumirizanso kuti atipatse kena kalikonse.+ Tichita ndendende mmene wanenera.”+ Choncho ndinaitana ansembe ndi kulumbiritsa olakwawo kuti achite mogwirizana ndi mawu amenewa.+ 13  Kuwonjezera apo, ndinakutumula zovala zanga, kenako ndinati: “Mofanana ndi zimenezi, Mulungu woona akutumule munthu aliyense wosachita mogwirizana ndi mawu amenewa, kum’chotsa m’nyumba yake ndi pa zinthu zake zonse. Ndipo munthu wotero akutumulidwe mwa njira imeneyi ndi kukhala wopanda kalikonse.” Pamenepo mpingo wonse unati: “Zikhale momwemo!”*+ Ndipo anayamba kutamanda Yehova.+ Choncho anthuwo anachitadi mogwirizana ndi mawu amenewa.+ 14  Chinanso: Kwa zaka 12, kuchokera tsiku limene anandiika kukhala bwanamkubwa wawo+ m’dziko la Yuda, m’chaka cha 20+ mpaka m’chaka cha 32+ cha mfumu Aritasasita,+ ine ndi abale anga sitinadye chakudya choyenera kuperekedwa kwa bwanamkubwa.+ 15  Abwanamkubwa amene analipo ine ndisanakhale, ankalemetsa anthu, ndipo tsiku ndi tsiku anali kulandira masekeli* 40 a siliva kuti akagule chakudya ndi vinyo. Komanso atumiki awo anali kupondereza anthu.+ Koma ine sindinachite zimenezo+ chifukwa choopa Mulungu.+ 16  Kuwonjezera apo, ndinagwira nawo ntchito yomanga mpandawo+ ndipo sitinakhale ndi minda.+ Atumiki anga onse anasonkhana pamodzi kumeneko kuti agwire ntchito. 17  Ayuda ndi atsogoleri, amuna okwana 150, pamodzi ndi anthu obwera kwa ife kuchokera ku mitundu yotizungulira anali kudya nafe limodzi.+ 18  Tsiku lililonse ndinali kuuza anthu kuti akonze ng’ombe imodzi yamphongo, nkhosa zosankhidwa mwapadera 6 ndi mbalame. Ndipo kamodzi pa masiku 10 alionse ndinali kupereka vinyo wochuluka wamtundu uliwonse.+ Kuwonjezera pamenepo, sindinapemphe kuti andipatse chakudya choyenera kuperekedwa kwa bwanamkubwa chifukwa utumiki umene anthuwa anali kuchita unali wolemetsa. 19  Mulungu wanga, mundikumbukire+ pa zabwino+ zonse zimene ndachitira anthu awa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “Ame!” m’Chiheberi.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.