Nehemiya 3:1-32

3  Ndiyeno Eliyasibu+ mkulu wa ansembe ndi abale ake, ansembe, anayamba kumanga Chipata cha Nkhosa.+ Iwo anapatula mbali imeneyi+ ndi kuika zitseko zake. Anapatula mbali imeneyi mpaka ku Nsanja ya Meya+ ndi Nsanja ya Hananeli.+  Amuna a ku Yeriko+ nawonso anamanga kuyambira pamene Eliyasibu ndi abale ake analekezera. Kenako, Zakuri mwana wamwamuna wa Imiri, anamanga kuyambira pamene amuna a ku Yeriko analekezera.  Ana aamuna a Haseneya anamanga Chipata cha Nsomba.+ Iwo anachipangira felemu lamatabwa+ ndi kuika zitseko zake,+ akapichi ake ndi mipiringidzo yake.+  Ndiyeno Meremoti+ mwana wamwamuna wa Uliya,+ mwana wamwamuna wa Hakozi, anakonza mpandawo kuchokera pamene ana aamuna a Haseneya analekezera. Kenako, Mesulamu+ mwana wamwamuna wa Berekiya, mwana wamwamuna wa Mesezabele, anakonza mpandawo kuchokera pamene Meremoti analekezera. Kenako, Zadoki mwana wamwamuna wa Baana, anakonza mpandawo kuchokera pamene Mesulamu analekezera.  Ndiyeno Atekowa+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Zadoki analekezera. Koma anthu otchuka pakati pa Atekowa+ sanagonjere ambuye awo ndi kuwatumikira.  Ndiyeno Yoyada mwana wamwamuna wa Paseya, komanso Mesulamu mwana wamwamuna wa Besodeya, anakonza Chipata cha Mzinda Wakale.+ Iwo anachipangira felemu lamatabwa ndi kuika zitseko zake, akapichi ake ndi mipiringidzo yake.+  Kenako Melatiya Mgibeoni+ ndi Yadoni Mmeronoti+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Yoyada ndi Mesulamu analekezera. Amenewa anali amuna a ku Gibeoni+ ndi Mizipa+ amene anali pansi pa ulamuliro wa bwanamkubwa+ wa kutsidya la Mtsinje.+  Kenako Uziyeli mwana wamwamuna wa Harihaya, mmodzi wa osula golide,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene winayo analekezera. Ndiyeno Hananiya mmodzi wa opanga mafuta onunkhira,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Uziyeli analekezera. Iwo anayala miyala mu Yerusalemu mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+  Kenako Refaya mwana wamwamuna wa Hura, kalonga wa hafu ya chigawo cha Yerusalemu, anakonza mpandawo kuchokera pamene Hananiya analekezera. 10  Ndiyeno Yedaya mwana wamwamuna wa Harumafi anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake+ kuchokera pamene Refaya analekezera. Kenako Hatusi mwana wamwamuna wa Hasabineya anakonza mpandawo kuchokera pamene Yedaya analekezera. 11  Malikiya mwana wamwamuna wa Harimu,+ komanso Hasubu mwana wamwamuna wa Pahati-mowabu,+ anakonza gawo lina la mpandawo, ndipo anakonzanso Nsanja ya Mauvuni.+ 12  Kenako Salumu mwana wamwamuna wa Halohesi, kalonga+ wa hafu ya chigawo cha Yerusalemu, anakonza mpandawo pamodzi ndi ana ake aakazi kuchokera pamene winayo analekezera. 13  Hanuni ndi anthu okhala ku Zanowa+ anakonza Chipata cha Kuchigwa.+ Iwo anachimanga ndi kuika zitseko zake,+ akapichi ake+ ndi mipiringidzo yake.+ Iwo anakonzanso mpandawo mikono* 1,000 mpaka kukafika ku Chipata cha Milu ya Phulusa.+ 14  Malikiya mwana wamwamuna wa Rekabu, kalonga wa chigawo cha Beti-hakeremu,+ anakonza Chipata cha Milu ya Phulusa. Iye anachimanga ndi kuika zitseko zake, akapichi ake ndi mipiringidzo yake. 15  Saluni mwana wamwamuna wa Kolihoze, kalonga wa chigawo cha Mizipa,+ anakonza Chipata cha Kukasupe.+ Iye anachimanga ndi kukhoma denga* lake. Anaikanso zitseko zake,+ akapichi ake ndi mipiringidzo yake. Iye anamanganso mpanda wa Dziwe+ la Ngalande* kukafika ku Munda wa Mfumu+ ndi ku Masitepe+ ochokera ku Mzinda wa Davide.+ 16  Ndiyeno Nehemiya mwana wamwamuna wa Azibuki, kalonga wa hafu ya chigawo cha Beti-zuri,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Saluni analekezera, kukafika patsogolo pa Manda Achifumu+ a Davide* ndi kudziwe+ lochita kukumba, mpaka kukafikanso ku Nyumba ya Anthu Amphamvu.+ 17  Ndiyeno Alevi,+ moyang’aniridwa ndi Rehumu mwana wamwamuna wa Bani,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Nehemiya analekezera. Hasabiya, kalonga wa hafu ya chigawo cha Keila,+ anakonza mpanda kuimira chigawo chake kuchokera pamene Alevi analekezera. 18  Abale awo anakonza mpandawo kuchokera pamenepo moyang’aniridwa ndi Bavai mwana wamwamuna wa Henadadi, kalonga wa hafu ya chigawo cha Keila. 19  Ndiyeno Ezeri mwana wamwamuna wa Yesuwa,+ kalonga wa Mizipa,+ anakonza gawo lina la mpandawo pafupi ndi chikweza chimene anthu amadutsa popita Kosungira Zida pa Mchirikizo wa Khoma.+ 20  Kenako, Baruki mwana wamwamuna wa Zabai,+ anagwira ntchito mwachangu kwambiri+ ndi kukonza gawo lina la mpandawo, kuchokera pa Mchirikizo wa Khoma kukafika pachipata cha nyumba ya Eliyasibu+ mkulu wa ansembe. 21  Kenako, Meremoti mwana wamwamuna wa Uliya,+ mwana wamwamuna wa Hakozi, anakonza gawo lina la mpandawo kuchokera pachipata cha nyumba ya Eliyasibu mpaka polekezera nyumbayo. 22  Ndiyeno ansembe, amuna a ku Chigawo* cha Yorodano+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Meremoti analekezera. 23  Kenako, Benjamini ndi Hasubu anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yawo kuchokera pamene ansembe analekezera. Kenako, Azariya mwana wamwamuna wa Maaseya, mwana wamwamuna wa Ananiya, anakonza mpandawo pafupi ndi nyumba yake kuchokera pamene Benjamini ndi Hasubu analekezera. 24  Kenako, Binui mwana wamwamuna wa Henadadi anakonza gawo lina la mpandawo kuchokera panyumba ya Azariya kukafika ku Mchirikizo wa Khoma+ ndi kukona ya mpanda wa mzindawo. 25  Ndiyeno Palali mwana wamwamuna wa Uzai, anakonza mpandawo kutsogolo kwa Mchirikizo wa Khoma ndipo anakonzanso nsanja yochokera pa Nyumba ya Mfumu+ imene ili kumtunda m’Bwalo la Alonda.+ Kenako, Pedaya mwana wamwamuna wa Parosi,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Palali analekezera. 26  Anetini+ anali kukhala ku Ofeli.+ Iwonso anakonza mpandawo mpaka kukafika ku Chipata cha Kumadzi,+ kum’mawa. Iwo anakonzanso nsanja yotundumukira kunja kwa mpanda. 27  Kenako, Atekowa+ anakonza chigawo chinanso cha mpandawo, kuchokera patsogolo pa nsanja yaikulu yotundumukira kunja kwa mpanda ija mpaka kukafika kumpanda wa Ofeli. 28  Ansembe anakonza mpandawo kuyambira kumtunda kwa Chipata cha Hatchi,+ ndipo aliyense anali kukonza patsogolo pa nyumba yake. 29  Kenako, Zadoki+ mwana wamwamuna wa Imeri, anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake. Ndiyeno, Semaya mwana wamwamuna wa Sekaniya, woyang’anira Chipata cha Kum’mawa,+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Zadoki analekezera. 30  Hananiya mwana wamwamuna wa Selemiya ndi Hanuni mwana wamwamuna wa 6 wa Zalafi, anakonzanso chigawo china cha mpanda. Kenako Mesulamu+ mwana wamwamuna wa Berekiya, anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba* yake kuchokera pamene winayo analekezera.+ 31  Malikiya amene anali m’gulu la osula golide,+ anakonza mpandawo mpaka kukafika kunyumba ya Anetini+ ndi amalonda,+ kutsogolo kwa Chipata cha Kufufuza* mpaka pachipinda chapadenga cha pakona. 32  Ndiyeno osula golide ndi amalonda anakonza mpandawo kuyambira pachipinda chapadenga cha pakona kukafika pa Chipata cha Nkhosa.+

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Kapena kuti “tsindwi.”
Kapena kuti “Dziwe la Sela.”
Zikuoneka kuti amenewa ndi manda a Davide ndi mafumu a Yuda amene anabwera pambuyo pake.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.
Kapena kuti “chipinda chachikulu.”
Kapena kuti “Chipata cha Hamifikadi.”