Nehemiya 2:1-20

2  Ndiyeno tsiku lina m’mwezi wa Nisani,*+ m’chaka cha 20+ cha mfumu Aritasasita,+ mfumuyo inali kufuna vinyo. Pamenepo ine ndinatenga vinyoyo ndi kum’pereka kwa mfumu monga mwa nthawi zonse.+ Koma ndinali ndisanakhalepo wachisoni pamaso pake.+  Ndiyeno mfumu inati: “N’chifukwa chiyani nkhope yako ili yachisoni+ pamene sukudwala? Pali chinachake chimene chikukuvutitsa mumtima.”+ Atanena zimenezi ndinachita mantha kwambiri.  Pamenepo ndinayankha mfumuyo kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!+ Kodi nkhope yanga ilekerenji kukhala yachisoni pamene mzinda+ umene makolo anga+ anaikidwako uli bwinja ndipo zipata zake zinatenthedwa ndi moto?”+  Poyankha, mfumuyo inandifunsa kuti: “Ndiye ukufuna chiyani?”+ Nthawi yomweyo ndinapemphera+ kwa Mulungu wakumwamba.+  Kenako ndinauza mfumu kuti: “Ngati zili bwino ndi inu mfumu,+ ndipo ngati ine mtumiki wanu mungandikomere mtima,+ munditumize ku Yuda, kumzinda umene makolo anga anaikidwako kuti ndikaumangenso.”+  Mfumu inandiyankha kuti: “Ulendo wako udzatenga masiku angati, ndipo udzabwera liti?” Pa nthawiyi, mkazi wamkulu wa mfumu anali atakhala pambali pake. Choncho mfumu inandilola kupita nditaiuza nthawi.+  Ndiyeno ndinauzanso mfumu kuti: “Ngati zili bwino ndi inu mfumu, lolani kuti ndipatsidwe makalata+ okasonyeza kwa abwanamkubwa+ a tsidya lina la Mtsinje,*+ kuti akandilole kudutsa ndi kukafika ku Yuda.  Komanso andipatse kalata yopita kwa Asafu amene akuyang’anira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokamangira zipata za Nyumba ya Chitetezo Champhamvu+ ya kukachisi,+ mpanda+ wa mzindawo ndiponso nyumba imene ndizikakhalamo.” Choncho mfumu inandipatsa makalatawo, chifukwa Mulungu anandikomera mtima.+  Pambuyo pake ndinafika kwa abwanamkubwa+ kutsidya lina la Mtsinje ndi kuwapatsa makalata a mfumu. Kuwonjezera apo, mfumu inandipatsa akuluakulu a gulu lankhondo ndi asilikali okwera pamahatchi* kuti ndiyende nawo. 10  Sanibalati+ wa ku Beti-horoni+ ndi Tobia,+ mtumiki wachiamoni,+ atamva zimenezi anaipidwa kwambiri+ kuti kwabwera munthu wofunira ana a Isiraeli zabwino. 11  Patapita nthawi, ndinafika ku Yerusalemu ndipo ndinakhala kumeneko masiku atatu. 12  Ndiyeno ndinadzuka usiku pamodzi ndi amuna angapo amene ndinali nawo. Sindinauze munthu aliyense+ zimene Mulungu wanga anali kuika mumtima mwanga zoti ndichitire Yerusalemu,+ ndipo ndinalibe chiweto chilichonse kupatulapo chiweto chimene ndinakwerapo. 13  Usikuwo ndinatulukira pa Chipata cha Kuchigwa,+ kutsogolo kwa Kasupe wa Chinjoka Chachikulu* ndi kulowera ku Chipata cha Kumilu ya Phulusa.+ Pa nthawiyi, ndinali kuonetsetsa+ mmene mpanda wa Yerusalemu unawonongekera ndiponso mmene moto unawonongera zipata zake.+ 14  Ndinayendabe mpaka kukafika ku Chipata cha Kukasupe+ ndi ku Dziwe la Mfumu, ndipo kumeneko kunalibe njira imene chiweto chimene ndinakwerapo chikanadutsa. 15  Koma usikuwo ndinayendabe mokwezeka m’chigwamo+ ndipo ndinapitirizabe kuonetsetsa mpandawo. Kenako ndinabwerera ndi kukalowanso pa Chipata cha Kuchigwa.+ 16  Atsogoleri+ a kumeneko sanadziwe kumene ndapita ndi zimene ndinali kuchita. Komanso Ayuda pamodzi ndi ansembe, anthu olemekezeka, atsogoleri ndi ena onse amene akanagwira ntchito yomanga mpanda ndinali ndisanawauze kalikonse. 17  Pamapeto pake ndinawauza kuti: “Inu mukuona vuto lalikulu limene tili nalo. Mukuona kuti Yerusalemu ali bwinja ndipo zipata zake zinatenthedwa ndi moto. Tiyeni timange mpanda wa Yerusalemu kuti anthu asiye kutitonza.”+ 18  Ndinawauzanso mmene dzanja+ la Mulungu wanga lachitira zinthu zabwino kwa ine+ ndiponso mawu amene mfumu inandiuza.+ Pamenepo iwo anati: “Tiyeni timange mpandawo.” Choncho analimbitsa manja awo kuti agwire ntchito yabwinoyi.+ 19  Ndiyeno Sanibalati+ wa ku Beti-horoni, Tobia+ mtumiki+ wachiamoni+ ndi Gesemu+ Mluya+ atamva zimenezi anayamba kutinyoza+ ndi kutiyang’ana moipidwa. Iwo anati: “N’chiyani chimene mukuchitachi? Kodi mukupandukira mfumu?”+ 20  Koma ine ndinawayankha kuti: “Mulungu wakumwamba+ ndi amene adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino,+ ndipo ife atumiki ake tipitiriza kumanga mpandawu. Inu mulibe gawo,+ ufulu kapena chilichonse chokukumbukirani nacho+ mu Yerusalemu.”

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 13.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Mwina amenewa anali malo amene anali kutchedwanso kuti Chitsime cha Eni-rogeli.