Nehemiya 11:1-36

11  Tsopano akalonga+ a anthuwo anali kukhala m’Yerusalemu.+ Anthu ena onse anachita maere+ kuti apeze munthu mmodzi mwa anthu 10 alionse woti akakhale m’Yerusalemu, mzinda woyera,+ ndiponso kuti anthu ena 9 otsalawo akhale m’mizinda ina.  Komanso, anthu anadalitsa+ amuna onse amene anadzipereka+ kukakhala m’Yerusalemu.  Otsatirawa ndiwo atsogoleri a m’chigawo cha Yuda+ amene anali kukhala m’Yerusalemu,+ koma m’mizinda ya Yuda munali kukhala ansembe,+ Alevi,+ Anetini+ ndi ana a atumiki a Solomo.+ Aliyense wa iwo anali kukhala m’malo ake m’mizinda yawo+ mu Isiraeli.+  Mu Yerusalemu munalinso kukhala ena mwa ana a Yuda ndi ena mwa ana a Benjamini.+ Mwa ana a Yuda panali Ataya mwana wamwamuna wa Uziya amene anali mwana wa Zekariya. Zekariya anali mwana wa Amariya, Amariya anali mwana wa Sefatiya, Sefatiya anali mwana wa Mahalalele wochokera m’banja la Perezi.+  Panalinso Maaseya mwana wa Baruki amene anali mwana wa Kolihoze. Kolihoze anali mwana wa Hazaya, Hazaya anali mwana wa Adaya, Adaya anali mwana wa Yoyaribi, Yoyaribi anali mwana wa Zekariya amene anali mwana wa Mshela.  Ana onse a Perezi amene anali kukhala mu Yerusalemu anali amuna amphamvu zawo okwana 468.  Ana aamuna a Benjamini+ anali awa: Salelu mwana wa Mesulamu,+ Mesulamu anali mwana wa Yoedi, Yoedi anali mwana wa Pedaya, Pedaya anali mwana wa Kolaya, Kolaya anali mwana wa Maaseya, Maaseya anali mwana wa Itiyeli, ndipo Itiyeli anali mwana wa Yesaiya.  Pambuyo pa Salelu panali Gabai ndi Salai ndipo onse pamodzi analipo 928.  Yoweli mwana wa Zikiri anali woyang’anira wawo ndipo Yuda mwana wa Hasenuwa anali wachiwiri kwa woyang’anira mzinda. 10  Pakati pa ansembe panali awa: Yedaya mwana wa Yoyaribi,+ Yakini,+ 11  Seraya mwana wa Hilikiya, Hilikiya anali mwana wa Mesulamu,+ Mesulamu anali mwana wa Zadoki,+ Zadoki anali mwana wa Merayoti, Merayoti anali mwana wa Ahitubu.+ Ahitubu anali mtsogoleri wa panyumba ya Mulungu woona. 12  Abale awo ogwira ntchito panyumbapo+ analipo 822. Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu.+ Yerohamu anali mwana wa Pelaliya, Pelaliya anali mwana wa Amuzi, Amuzi anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Pasuri,+ ndipo Pasuri anali mwana wa Malikiya.+ 13  Abale ake a Adaya, atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ analipo 242. Ndiyeno panalinso Amasisai mwana wa Azareli. Azareli anali mwana wa Azai, Azai anali mwana wa Mesilemoti amene anali mwana wa Imeri. 14  Amasisai pamodzi ndi abale ake, amuna amphamvu ndi olimba mtima,+ analipo okwana 128. Iwowa mtsogoleri+ wawo anali Zabidiyeli wochokera m’banja la anthu otchuka. 15  Pakati pa Alevi+ panali awa: Semaya mwana wa Hasubu. Hasubu anali mwana wa Azirikamu, Azirikamu anali mwana wa Hasabiya,+ ndipo Hasabiya anali mwana wa Buni. 16  Panalinso Sabetai+ ndi Yozabadi,+ mwa atsogoleri a Alevi. Amenewa anali kuyang’anira ntchito ya panja pa nyumba ya Mulungu woona. 17  Mataniya+ mwana wa Mika amene anali mwana wa Zabidi mwana wa Asafu,+ anali wotsogolera nyimbo zotamanda+ Mulungu. Iye anali kutamanda Mulungu pa nthawi ya mapemphero.+ Bakibukiya anali wachiwiri kwa woyang’anira pakati pa abale ake. Panalinso Abada mwana wa Samuwa, Samuwa anali mwana wa Galali, ndipo Galali+ anali mwana wa Yedutuni.+ 18  Alevi onse mumzinda woyera+ analipo 284. 19  Alonda a pazipata+ anali Akubu, Talimoni,+ ndi abale awo amene anali kulondera m’zipata.+ Onse pamodzi analipo 172. 20  Aisiraeli ena onse, komanso ansembe ndi Alevi ena onse, anali m’mizinda ina ya Yuda, aliyense pacholowa chake.+ 21  Anetini+ anali kukhala ku Ofeli,+ ndipo Ziha ndi Gisipa anali kuyang’anira Anetiniwo. 22  Woyang’anira+ Alevi pa ntchito ya panyumba ya Mulungu woona mu Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani. Bani anali mwana wa Hasabiya, Hasabiya anali mwana wa Mataniya,+ Mataniya anali mwana wa Mika+ wa m’banja la Asafu.+ A m’banja la Asafu anali oimba.+ 23  Mfumu inapereka lamulo lokhudza oimba,+ ndipo panali dongosolo loti aziwapatsa thandizo tsiku lililonse malinga ndi zofunikira za tsikulo.+ 24  Petahiya mwana wa Mesezabele, wa m’banja la Zera mwana wa Yuda, anali wothandiza mfumu pa nkhani zonse zokhudza anthu. 25  Ana ena a Yuda anali kukhala m’midzi ndi m’madera ozungulira midziyo.+ Ena anali kukhala ku Kiriyati-ariba+ ndi midzi yake yozungulira, ku Diboni* ndi midzi yake yozungulira, ku Yekabizeeli+ ndi midzi yake yozungulira, 26  ku Yesuwa, ku Molada,+ ku Beti-peleti,+ 27  ku Hazara-suali,+ ku Beere-seba+ ndi midzi yake yozungulira, 28  ku Zikilaga,+ ku Mekona ndi midzi yake yozungulira, 29  ku Eni-rimoni,+ ku Zora,+ ku Yarimuti,+ 30  ku Zanowa,+ ku Adulamu+ ndi midzi yake yozungulira, ku Lakisi+ ndi madera ake ozungulira, ku Azeka+ ndi midzi yake yozungulira. Iwo anamanga misasa kuyambira ku Beere-seba mpaka kuchigwa cha Hinomu.+ 31  Ana a Benjamini anakhala ku Geba,+ Mikimasi,+ Aiya,+ Beteli+ ndi midzi yake yozungulira, 32  ku Anatoti,+ Nobu,+ Ananiya, 33  Hazori, Rama,+ Gitaimu,+ 34  Hadidi, Zeboyimu, Nebalati, 35  Lodi,+ Ono+ ndi kuchigwa cha amisiri. 36  Ndipo ena mwa Alevi a ku Yuda anakakhala ku Benjamini.

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti malowa ndi amodzimodzi ndi “Dimona” wotchulidwa pa Yos 15:22.