Nahumu 3:1-19

3  Tsoka mzinda wokhetsa magazi.+ Mzindawo wadzaza ndi chinyengo ndi chifwamba, moti nthawi zonse umafunkha zinthu za anthu ena.  Kukumveka kulira kwa mkwapulo,+ kulira kwa mawilo, mgugu wa mahatchi* ndi kudumpha kwa magaleta.+  Komanso pali asilikali okwera pamahatchi, malupanga a moto walawilawi, mikondo yowalima ngati mphezi,+ anthu ambiri ophedwa ndiponso mulu waukulu wa mitembo moti pena paliponse pali mitembo yosawerengeka. Anthu akupunthwa pamitembo ya anthu awo.  Zimenezi zili choncho chifukwa cha kuchuluka kwa zochita zake zauhule+ ndi kukongola kwake kochititsa kaso. Iye ndi mkazi waluso lamatsenga ndipo amakopa mitundu ya anthu ndi zochita zake zauhule, amakopa mitundu ya anthu ndi zochita zake zamatsenga.+  Yehova wa makamu wanena kuti: “Taona! Ine ndikukuukira,+ ndipo ndidzakuvula siketi yako ndi kukuphimba nayo kumaso moti ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ione maliseche ako+ ndi kutinso maufumu aone manyazi ako.  Ndidzakuponyera zinthu zonyansa+ ndipo ndidzakuchititsa kukhala chinthu chonyozeka ndiponso choopsa.+  Aliyense wokuona adzakuthawa+ ndipo adzanena kuti, ‘Nineve wasakazidwa! Ndani adzamuchitira chisoni?’ Kodi anthu oti akutonthoze ndiwapeza kuti?  Kodi iwe uli pabwino kuposa No-amoni+ amene anali pafupi ndi ngalande zochokera mumtsinje wa Nailo?+ Iye anali wozunguliridwa ndi madzi. Chuma chake chinali kuchokera m’nyanja, ndipo nyanjayo ndiyo inali khoma lake.  Mphamvu zake zonse zinali kuchokera ku Itiyopiya komanso ku Iguputo,+ ndipo zinali zopanda malire. Anthu a ku Puti komanso a ku Libiya anali kumuthandiza.+ 10  Koma nayenso No-amoni anayenera kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndipo anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo. Ana ake anaphwanyidwaphwanyidwa m’misewu yake yonse+ ndipo anthu ake olemekezeka anawachitira maere.+ Anthu ake onse otchuka anamangidwa m’matangadza.+ 11  “Chotero iwenso udzaledzera,+ ndipo udzabisala.+ Iwenso udzafunafuna malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri kuti utetezeke kwa mdani.+ 12  Malo ako onse okhala ndi mpanda wolimba kwambiri ali ngati mitengo ya mkuyu imene ili ndi nkhuyu zoyambirira kupsa. Munthu akagwedeza mitengoyo, nkhuyu zakezo zimagwera m’kamwa mwa munthu wozidya.+ 13  “Taona! Anthu ako ali ngati akazi.+ Zipata za dziko lako zidzatsegulidwa kuti adani ako alowemo. Moto udzanyeketsa mipiringidzo ya mzinda wako.+ 14  Tunga madzi kuti upange chiunda chomenyerapo nkhondo.*+ Limbitsa malo ako okhala ndi mpanda wolimba kwambiri.+ Lowa m’matope ndi kupondaponda dothi. Gwira chikombole. 15  Koma ngakhale utero, moto udzakunyeketsa. Lupanga lidzakuduladula+ ndipo lidzakudya ngati mmene ana a dzombe oyenda pansi amadyera zomera.+ Dzichulukitseni ngati ana a dzombe oyenda pansi, dzichulukitseni ngati dzombe. 16  Iwe wachulukitsa anthu ako amalonda kuposa nyenyezi zakumwamba.+ “Ana a dzombe oyenda pansi amafundula ndipo kenako amaulukira kutali. 17  Alonda ako ali ngati dzombe ndipo akapitawo ako olemba anthu usilikali ali ngati gulu la dzombe. Pa tsiku lozizira limabisala m’makoma. Dzuwa likawala, dzombelo limauluka ndi kuthawira kutali ndipo silidziwika kuti lili kuti.+ 18  “Abusa ako ayamba kuwodzera,+ iwe mfumu ya Asuri, ndipo anthu ako olemekezeka akungokhala m’nyumba zawo.+ Anthu ako amwazikana pamapiri ndipo palibe amene akuwasonkhanitsa pamodzi.+ 19  Masoka ako sadzakupatsa mpata wopuma. Chilonda chako chakhala chosachiritsika.+ Kodi pali amene sunamuvutitse ndi zoipa zako nthawi zonse?+ N’chifukwa chake onse amene adzamva za iwe adzakuwombera m’manja.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.