Nahumu 2:1-13

2  Womwaza wafika pamaso pako.+ Teteza malo amene ali ndi mpanda wolimba kwambiri. Londera njira yako. Konzekera kumenya nkhondo.* Kunga mphamvu zako zonse.+  Pamenepo Yehova adzakweza ulemu wa Yakobo+ ndi kubwezeretsa ulemerero wa Isiraeli. Pakuti owononga awawononga,+ ndipo mphukira zawo zasakazidwa.+  Amuna amphamvu ovala zovala zofiira kwambiri afika. Anyamula zishango zonyika mu ututo wofiira.+ Pokonzekera nkhondo, iwo akukweza mikondo yawo yokhala ndi zogwirira zamtengo.+ Zida zawo zankhondo zachitsulo zimene zili pamagaleta awo zili waliwali ngati moto.  Magaleta awo ankhondo akuyenda mothamanga kwambiri m’misewu.+ Iwo akuthamangira uku ndi uku m’mabwalo a mzinda, ndipo akuoneka ngati zounikira zamoto. Magaletawo akuderukaderuka ngati mphezi.+  Mfumu idzakumbukira asilikali ake amphamvu.+ Iwo adzathamangira kumpanda wa mzinda ndipo pamene akutero adzakhala akupunthwa.+ Pamenepo mpanda wachitetezo udzakhala ndi chitetezo champhamvu.  Zotsekera madzi a m’mitsinje zidzatsegulidwa, ndipo nyumba yachifumu idzawonongedwa.  Nkhani imeneyi yatsimikiziridwa. Mzindawo udzavulidwa ndi kuchititsidwa manyazi, ndipo anthu ake adzatengedwa.+ Akapolo ake aakazi adzakhala akulira ngati nkhunda+ ndipo adzadziguguda pachifuwa.+  Kuchokera pamene Nineve anakhalapo,+ iye wakhala ngati dziwe la madzi,+ koma tsopano anthu ake akuthawa. Ena akufuula kuti: “Imani amuna inu! Imani!” Koma palibe amene akubwerera.+  Funkhani siliva amuna inu, funkhani golide,+ pakuti iwo ali ndi zinthu zochuluka kwambiri. Ali ndi zinthu zosiririka zosiyanasiyana zadzaoneni.+ 10  Mzindawu auchititsa kukhala wopanda kanthu ndipo ausandutsa bwinja.+ Mitima yawo yasungunuka ndi mantha.+ Mawondo awo akunjenjemera+ ndipo akumva ululu thupi lonse.+ Nkhope zawo zonse zili ndi nkhawa.+ 11  Kodi malo obisalamo mikango, phanga la mikango yamphamvu, malo amene mkango unali kuyenda ndi kulowa,+ malo amene munali mwana wa mkango, mmene mikango inali kukhala popanda woiwopsa, ali kuti?+ 12  Mkango unali kukhadzulakhadzula nyama yokwanira kuti udyetse ana ake ndipo unali kupha nyama kuti upatse mikango yaikazi. Mapanga ake anali kukhala odzaza ndi nyama, ndipo malo ake obisalamo anali ndi nyama zokhadzulakhadzula.+ 13  Yehova wa makamu akuti, “Taona! Ine ndikukuukira,+ ndipo nditentha magaleta ako ankhondo moti padzakhala utsi wambiri.+ Lupanga lidzadya mikango yako yamphamvu.+ Sudzasakanso nyama padziko lapansi,* ndipo mawu a amithenga ako sadzamvekanso.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Limbitsa chiuno chako.”
Mawu ake enieni, “Ndidzadula nyama zimene umagwira padziko lapansi.”