Mlaliki 9:1-18

9  Ine ndinafuna kumvetsetsa ndi kuganizira mozama zinthu zonsezi:+ Anthu olungama ndiponso anthu anzeru limodzi ndi ntchito zawo ali m’dzanja la Mulungu woona.+ Anthu sadziwa za chikondi kapena chidani chimene chinalipo iwo asanakhalepo.+  Zimene zimachitikira anthu onse n’zofanana.+ Pali mapeto amodzi+ kwa munthu wolungama+ ndi woipa,+ kwa munthu wabwino, woyera, ndi wodetsedwa, ndiponso kwa munthu amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe. Munthu wabwino n’chimodzimodzi ndi munthu wochimwa.+ Munthu amene amalumbira mosaganizira bwino n’chimodzimodzi ndi amene amaopa kulumbira.+  Chimene chimamvetsa chisoni pa zinthu zonse zimene zimachitika padziko lapansi pano n’chakuti, popeza mapeto a anthu onse ndi amodzi,+ mtima wa ana a anthu ndi wodzazanso ndi zoipa.+ Mumtima mwawo mumakhala misala+ pa nthawi imene ali ndi moyo ndipo pamapeto pake, iwo amapita kwa akufa.+  Aliyense amene ali pakati pa anthu amoyo ali ndi chiyembekezo, chifukwa galu wamoyo+ ali bwino kuposa mkango wakufa.+  Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse.+ Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika.+  Komanso chikondi chawo, chidani chawo ndiponso nsanje yawo zatha kale,+ ndipo alibenso gawo mpaka kalekale pa chilichonse chimene chikuchitika padziko lapansi pano.+  Pita ukadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala,+ chifukwa Mulungu woona wakondwera kale ndi ntchito zako.+  Nthawi zonse zovala zako zizikhala zoyera,+ ndipo pamutu pako pasamasowe mafuta.+  Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi wako amene umamukonda+ masiku onse a moyo wako wachabechabe, amene Mulungu wakupatsa padziko lapansi pano. Usangalale masiku ako onse achabechabe, pakuti imeneyo ndiyo mphoto yako pamoyo,+ ndi pa ntchito yovuta imene ukuigwira mwakhama padziko lapansi pano. 10  Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse,+ pakuti kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu,+ kapena nzeru,+ ku Manda*+ kumene ukupitako.+ 11  Nditaganizanso ndinaona kuti padziko lapansi pano anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano,+ amphamvu sapambana pankhondo,+ anzeru sapeza chakudya,+ omvetsa zinthu nawonso sapeza chuma,+ ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa,+ chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.+ 12  Pakuti munthu+ nayenso sadziwa nthawi yake.+ Monga nsomba zimene zagwidwa mu ukonde wakupha,+ ndi mbalame zimene zakodwa mumsampha,+ ana a anthu nawonso amakodwa pa nthawi yatsoka,+ nthawiyo ikawafikira mwadzidzidzi.+ 13  Padziko lapansi pano ndinaonapo nzeru izi, zimene zinali zogometsa kwa ine: 14  Panali mzinda winawake waung’ono ndipo mumzindamo munali amuna ochepa. Kenako kunabwera mfumu yamphamvu ndipo inazungulira mzindawo, n’kuunjika milu ikuluikulu yadothi yoti imenyerepo nkhondo.+ 15  Mumzindawo munali munthu wina wosauka koma wanzeru, amene anapulumutsa mzindawo chifukwa cha nzeru zake.+ Koma kenako palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo.+ 16  Choncho ineyo ndinati: “Nzeru n’zabwino kuposa mphamvu,+ koma nzeru za munthu wosauka zimanyozedwa ndipo anthu samvera mawu ake.”+ 17  Mawu otsitsa a anthu anzeru amamveka kwambiri+ kuposa kukuwa kwa munthu amene akulamulira pakati pa anthu opusa.+ 18  Ndi bwino kukhala ndi nzeru kuposa kukhala ndi zida zomenyera nkhondo, ndipo wochimwa mmodzi yekha akhoza kuwononga zabwino zochuluka.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 5.