Mlaliki 8:1-17
8 Ndani angafanane ndi munthu wanzeru?+ Ndipo ndani amadziwa kumasulira zinthu?+ Nzeru za munthu zimachititsa nkhope yake kuwala ndipo ngakhale nkhope yake yokwiya imasintha n’kumaoneka bwino.+
2 Ndikunena kuti: “Sunga lamulo la mfumu.+ Chita zimenezi polemekeza lumbiro la Mulungu.+
3 Usafulumire kuchoka pamaso pake,+ ndipo usayambe kuchita zoipa.+ Pakuti mfumuyo idzachita zonse zimene ikufuna kuchita,+
4 chifukwa mawu a mfumu ali ndi mphamvu yolamulira,+ ndipo ndani angaifunse kuti: ‘Kodi mukuchita chiyani?’”
5 Wosunga malamulo sadzakumana ndi tsoka lililonse,+ ndipo mtima wanzeru udzadziwa nthawi ndi chiweruzo.+
6 Chochitika chilichonse chili ndi nthawi yake ndi chiweruzo chake,+ chifukwa mavuto a anthu ndi ambiri.+
7 Pakuti palibe akudziwa zimene zidzachitike,+ popeza ndani angamuuze mmene zidzachitikire?
8 Palibe munthu amene ali ndi mphamvu pa mzimu kuti auletse mzimuwo.+ Palibenso amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa.+ Palibe amene samenya nawo nkhondo,+ ndipo kuchita zoipa sikudzapulumutsa amene amachita zoipawo.+
9 Zonsezi ndaziona ndipo mtima wanga unaganizira za ntchito iliyonse imene yachitidwa padziko lapansi pano, pa nthawi imene munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.+
10 Koma ngakhale zili choncho, ndaona anthu oipa akuikidwa m’manda.+ Ndaonanso mmene iwo anabwerera ndi mmene anachokera pamalo oyera,+ n’kuiwalika mumzinda umene anali kuchitiramo zoipazo.+ Izinso n’zachabechabe.
11 Popeza anthu ochita zoipa sanalangidwe msanga,+ n’chifukwa chake mtima wa ana a anthu wakhazikika pa kuchita zoipa.+
12 Ngakhale woipa atachita zoipa+ maulendo 100 n’kukhala ndi moyo wautali akuchitabe zofuna zake, ine ndikudziwa kuti anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino,+ chifukwa chakuti anali kumuopa.+
13 Koma woipayo sizidzamuyendera bwino n’komwe,+ ndiponso sadzachulukitsa masiku ake amene ali ngati mthunzi,+ chifukwa saopa Mulungu.+
14 Pali chinthu china chachabe chimene chimachitika padziko lapansi: Pali anthu olungama amene amakumana ndi zinthu zimene amayenera kukumana nazo anthu oipa,+ ndiponso pali anthu oipa amene amakumana ndi zinthu zimene amayenera kukumana nazo anthu olungama.+ Ndinanena kuti zimenezinso n’zachabechabe.
15 Ineyo ndinatamanda kusangalala,+ chifukwa palibe chabwino chimene anthu angachite padziko lapansi pano kuposa kudya, kumwa ndi kusangalala, pamene akugwira ntchito mwakhama masiku onse a moyo wawo,+ amene Mulungu woona wawapatsa padziko lapansi pano.+
16 Mogwirizana ndi zimenezi ndinatsimikiza mumtima mwanga+ kuti ndidziwe nzeru ndiponso ndione ntchito imene ikuchitika padziko lapansi,+ chifukwa alipo amene sagona tulo usana ndi usiku.+
17 Ndinaona ntchito yonse ya Mulungu woona,+ ndipo ndinaona kuti anthu amalephera kudziwa ntchito imene yachitika padziko lapansi pano.+ Kaya anthu ayesetse bwanji kuifufuza, safika poidziwa.+ Ngakhale atanena kuti ali ndi nzeru zokwanira zodziwira zinthu,+ sangathe kuidziwa.+