Mlaliki 6:1-12

6  Pali zinthu zomvetsa chisoni zimene ndaona padziko lapansi pano, ndipo n’zofala pakati pa anthu:  Pali munthu amene Mulungu woona amam’patsa chuma, katundu, ndi ulemerero,+ ndiponso amene sasowa chilichonse chimene moyo wake umalakalaka,+ koma Mulungu woona samulola kudya zinthu zakezo,+ ndipo mlendo+ ndi amene amazidya. Zimenezi n’zachabechabe ndipo ndi nthenda yoipa.  Ngati munthu atabereka ana 100+ n’kukhala ndi moyo zaka zambirimbiri, masiku a moyo wake n’kukhala ochuluka,+ koma moyo wake osakhutira ndi zinthu zabwino,+ komanso osalowa m’manda,+ ndithu mwana amene anabadwa wakufa ali bwino kuposa iyeyu.+  Pakuti mwanayu anangobadwira pachabe. Iye anapita mu mdima ndipo dzina lake lidzaphimbidwa ndi mdima.+  Ngakhale dzuwa sanalione, kapena kulidziwa.+ Ameneyu ali ndi mpumulo kusiyana ndi woyamba uja.+  Ngakhale munthu atakhala ndi moyo zaka 2,000, koma sanasangalale ndi zabwino,+ kodi phindu lake n’chiyani? Pajatu aliyense amapita kumalo amodzi.+  Ntchito yonse imene anthu amaigwira mwakhama amagwirira pakamwa pawo,+ koma moyo wawo sukhuta.  Kodi munthu wanzeru amaposa bwanji munthu wopusa?+ Kodi munthu wovutika amapindula chiyani chifukwa chodziwa mmene angachitire zinthu ndi anthu?  Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima.+ Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.+ 10  Chilichonse chimene chinakhalapo chinapatsidwa kale dzina, ndipo zinadziwika kale kuti munthu ndi ndani.+ Iye sangathe kudziteteza pa mlandu wotsutsana ndi amene ali wamphamvu kuposa iyeyo.+ 11  Chifukwa chakuti pali zambiri zoyambitsa zinthu zachabe,+ kodi munthu amapindula chiyani? 12  Ndani angadziwe zabwino zimene munthu angachite pa moyo wake,+ masiku onse a moyo wake wachabechabe, umene umakhala ngati mthunzi?+ Pakuti ndani angamuuze munthu zimene zidzachitike padziko lapansi pano iyeyo atafa?+

Mawu a M'munsi