Mlaliki 4:1-16

4  Ine ndinaganiziranso kuponderezana+ konse kumene kukuchitika padziko lapansi pano, ndipo ndinaona misozi ya anthu amene akuponderezedwa,+ koma panalibe wowatonthoza.+ M’manja mwa oponderezawo munali mphamvu, moti oponderezedwawo analibe wowatonthoza.  Ndinazindikira kuti anthu amene anafa kale ali bwino kuposa anthu amene ali moyo.+  Koma amene ali bwino kuposa onsewa ndi amene sanabadwe,+ amene sanaone ntchito yosautsa mtima imene ikuchitika padziko lapansi pano.+  Ineyo ndaona ntchito yonse imene anthu amaigwira mwakhama ndiponso imene amaigwira bwino,+ kuti imabweretsa mpikisano pakati pa anthu.*+ Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.  Wopusa amapinda manja+ ake ndipo amadziwononga yekha.+  Kupuma pang’ono* kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama* ndi kuthamangitsa mphepo.+  Ine ndinaganiziranso zachabechabe zochitika padziko lapansi pano:  Pali munthu amene ali yekhayekha, wopanda mnzake.+ Alibenso mwana kapena m’bale wake,+ koma amangokhalira kugwira ntchito mwakhama. Komanso maso ake sakhutira ndi chuma.+ Iye amafunsa kuti: “Kodi ntchito yovutayi ndikugwirira ndani n’kumadzimana zinthu zabwino?”+ Izinso n’zachabechabe ndiponso ndi ntchito yosautsa mtima.+  Awiri amaposa mmodzi,+ chifukwa amapeza mphoto yabwino pa ntchito yawo imene amaigwira mwakhama.+ 10  Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.+ Koma kodi zingakhale bwanji munthu mmodzi atagwa popanda wina woti am’dzutse?+ 11  Komanso, anthu awiri akagona pamodzi, amamva kutentha. Koma kodi mmodzi yekha angamve bwanji kutentha?+ 12  Ngati wina angagonjetse munthu mmodzi, anthu awiri akhoza kulimbana naye.+ Ndipo chingwe chopotedwa ndi zingwe zitatu sichingaduke msanga. 13  Mwana wosauka koma wanzeru ali bwino+ kuposa mfumu yokalamba koma yopusa,+ imene sionanso kufunika kochenjezedwa.+ 14  Pakuti mwanayo amatuluka m’ndende n’kukhala mfumu,+ ngakhale kuti anabadwa ngati wosauka mu ufumuwo.+ 15  Ndaona anthu onse amoyo amene amayenda padziko lapansi pano. Ndaonanso mmene zimakhalira ndi mwana amene amalowa m’malo mwa mfumu.+ 16  Ngakhale kuti anthu amene anali kumbali yake anali ambiri,+ pambuyo pake sadzakhutira naye,+ pakuti zimenezinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “imachitika chifukwa cha mpikisano pakati pa anthu.”
Mawu ake enieni, “kupuma kodzaza dzanja limodzi.”
Mawu ake enieni, “ntchito yovuta yodzaza manja awiri.”