Mlaliki 3:1-22
3 Chilichonse chili ndi nthawi yake,+ ndipo chilichonse chochitika padziko lapansi chilidi ndi nthawi yake:
2 Pali nthawi yobadwa+ ndi nthawi ya kufa.+ Nthawi yobzala ndi nthawi yozula chimene chinabzalidwa.+
3 Nthawi yakupha+ ndi nthawi yochiritsa.+ Nthawi yogumula ndi nthawi yomanga.+
4 Nthawi yolira+ ndi nthawi yoseka.+ Nthawi yolira mofuula+ ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.+
5 Nthawi yotaya miyala+ ndi nthawi younjika miyala pamodzi.+ Nthawi yokumbatirana+ ndi nthawi yosakumbatirana.+
6 Nthawi yofunafuna+ ndi nthawi yovomereza kuti chinthu chatayika. Nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.+
7 Nthawi yong’amba+ ndi nthawi yosoka.+ Nthawi yokhala chete+ ndi nthawi yolankhula.+
8 Nthawi ya chikondi ndi nthawi ya chidani ndi munthu.+ Nthawi yankhondo+ ndi nthawi yamtendere.+
9 Kodi munthu wogwira ntchito mwakhama adzapeza phindu lanji pa ntchito yakeyo?+
10 Ndaona ntchito imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azigwira.+
11 Chilichonse iye anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake.+ Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale+ kuti ntchito imene Mulungu woona wagwira, iwo asaidziwe kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.+
12 Ndazindikira kuti palibe chabwino kuposa kuti iwo asangalale ndiponso azichita zabwino pamene ali ndi moyo,+
13 komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.+ Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+
14 Ndazindikira kuti zonse zimene Mulungu woona amapanga zimakhala mpaka kalekale.+ Palibe choti n’kuwonjezerapo kapena choti n’kuchotsapo.+ Mulungu woona ndi amene wapanga zimenezi,+ kuti anthu azimuopa.+
15 Zimene zilipo zinalipo kale, ndipo zimene zidzachitike zinachitikapo kale.+ Mulungu woona+ amafunafuna kuchitira zabwino anthu amene akuzunzidwa.+
16 Ine ndaonanso padziko lapansi pano kuti pamene panayenera kukhala chilungamo panali zoipa, ndipo pamene panayenera kuchitika zachilungamo panachitika zoipa.+
17 Ine ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Mulungu woona adzaweruza munthu wolungama ndi munthu woipa,+ pakuti iye ali ndi nthawi yochitira chinthu chilichonse ndiponso yokhudza ntchito iliyonse.”+
18 Ineyo ndinanena mumtima mwanga kuti Mulungu woona adzasankhula ana a anthu. Zimenezi zidzawasonyeza kuti iwo ndi ofanana ndi zinyama.+
19 Pakuti ana a anthu ali ndi mapeto, ndipo zinyamanso zili ndi mapeto. Mapeto a zonsezi ndi ofanana.+ Nyama imafa ndipo munthunso amafa.+ Mzimu wa zonsezi ndi umodzi,+ moti munthu saposa nyama, pakuti zonse n’zachabechabe.
20 Zonse zimapita kumalo amodzi.+ Zonse zinachokera kufumbi+ ndipo zonse zimabwerera kufumbi.+
21 Ndani akudziwa ngati mzimu* wa ana a anthu umakwera m’mwamba, ndiponso ngati mzimu wa zinyama umatsika pansi?+
22 Ine ndaona kuti palibe chabwino kuposa kuti munthu asangalale ndi ntchito yake,+ pakuti imeneyo ndi mphoto yake, popeza palibe amene adzam’bweretse kuti adzaone zimene zizidzachitika iye atafa.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 4.