Mlaliki 12:1-14

12  Kumbukira Mlengi wako Wamkulu+ masiku a unyamata wako,+ asanafike masiku oipa+ komanso zisanafike zaka zimene udzati: “Moyo sukundisangalatsa.”+  Uchite zimenezi kuwala kwa dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi kusanazime,+ ndiponso mitambo isanabwerere kuti igwetse mvula.  Pa nthawi imeneyo oyang’anira nyumba+ azidzanjenjemera, amuna amphamvu adzapindika,+ akazi opera ufa+ adzasiya kugwira ntchito chifukwa adzatsala ochepa, akazi oyang’ana pawindo+ azidzaona mdima,  zitseko zotulukira popita mumsewu zidzatsekedwa,+ phokoso la miyala yoperera ufa lidzayamba kumveka motsika,+ ndipo munthu azidzadzuka ndi kulira kwa mbalame, ndiponso ana onse aakazi azidzaimba nyimbo ndi mawu otsika.+  Komanso uzidzaopa chimene chili pamwamba ndipo m’njira mudzakhala zoopsa. Mtengo wa amondi udzachita maluwa,+ chiwala chizidzayenda mochita kudzikoka ndipo zakudya sizidzakoma,* popeza munthu adzakhala akupita kunyumba yake yokhalitsa+ ndipo olira azidzazungulira mumsewu.+  Umukumbukire, chingwe chasiliva chisanachotsedwe, mbale yagolide isanaphwanyidwe,+ mtsuko usanaphwanyike pakasupe, ndiponso wilo lotungira madzi pachitsime lisanathyoke.  Kenako fumbi lidzabwerera kunthaka+ kumene linali, ndipo mzimu*+ udzabwerera kwa Mulungu woona+ amene anaupereka.+  Wosonkhanitsa+ anati: “Zachabechabe! Zinthu zonse n’zachabechabe.”+  Kuwonjezera pa kukhala ndi nzeru,+ wosonkhanitsayo nthawi zonse anali kuphunzitsanso anthuwo kuti adziwe zinthu.+ Anali kusinkhasinkha ndi kufufuza zinthu mosamala,+ ndipo analemba miyambi yambiri m’ndondomeko yoyenera.+ 10  Wosonkhanitsayo anafufuza mawu okoma+ ndipo analemba mawu olondola a choonadi.+ 11  Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga zobayira ng’ombe pozitsogolera,+ ndipo anthu amene amadzipereka kusonkhanitsa mawu anzeru, ali ngati misomali yokhomerera kwambiri.+ Mawuwo aperekedwa ndi m’busa mmodzi.+ 12  Mwana wanga, ponena za chilichonse chowonjezera pa izi, ndikukuchenjeza kuti: Kupanga mabuku ambiri sikudzatha ndipo kuwawerenga kwambiri kumangotopetsa munthu.+ 13  Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita. 14  Pakuti Mulungu woona adzaweruza ntchito iliyonse ndiponso chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati zili zabwino kapena zoipa.+

Mawu a M'munsi

“Zakudya sizidzakoma.” Mawu ake enieni akufotokoza kuti chipatso cha mtundu winawake, chimene munthu amadya kuti zakudya ziyambirenso kumukomera, chaphulika.
Onani Zakumapeto 4.