Mlaliki 11:1-10
11 Tumiza mkate wako+ pamadzi,+ chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.+
2 Pereka gawo la zinthu zimene uli nazo kwa anthu 7, ngakhale 8,+ chifukwa sukudziwa tsoka limene lidzagwe padziko lapansi.+
3 Mitambo ikadzaza madzi, imakhuthulira mvula yochuluka padziko lapansi,+ ndipo mtengo+ ukagwera kum’mwera kapena kumpoto, pamene wagwerapo udzakhala pomwepo.
4 Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.+
5 Monga momwe sudziwira mmene mzimu umagwirira ntchito m’thupi la mwana amene ali m’mimba mwa mayi ake,+ momwemonso sudziwa ntchito ya Mulungu woona, amene amachita zinthu zonse.+
6 Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo,+ chifukwa sukudziwa pamene padzachite bwino,+ kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzachite bwino.
7 Kuwala n’kokoma ndipo ndi bwino kuti maso aone dzuwa.+
8 Ngakhale munthu atakhala ndi moyo zaka zambiri, m’zaka zonsezo azisangalala.+ Iye akumbukire masiku a mdima,+ ngakhale atakhala ambiri. Tsiku lililonse limene likubwera n’lachabechabe.+
9 Mnyamatawe, sangalala+ ndi unyamata wako, ndipo mtima wako ukusangalatse masiku a unyamata wako. Yenda m’njira za mtima wako ndiponso motsatira zimene maso ako akuona.+ Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza chifukwa cha zonsezi.+
10 Choncho chotsa zosautsa mumtima mwako ndipo teteza thupi lako ku tsoka,+ chifukwa unyamata ndiponso pachimake pa moyo n’zachabechabe.+