Mlaliki 10:1-20

10  Ntchentche zakufa n’zimene zimachititsa mafuta onunkhira oyengedwa bwino+ kuwola ndi kuyamba kununkha. Momwemonso uchitsiru pang’ono umawononga mbiri ya munthu amene akulemekezedwa chifukwa cha nzeru ndi ulemerero wake.+  Mtima wa munthu wanzeru uli kudzanja lake lamanja,+ koma mtima wa munthu wopusa uli kudzanja lake lamanzere.+  Komanso, m’njira iliyonse imene munthu wopusa amayenda,+ mtima wake umakhala wopanda nzeru, ndipo amauza aliyense kuti ndi wopusa.+  Mzimu wa mtsogoleri ukakuukira, usachoke pamalo ako,+ chifukwa kudekha kumachepetsa machimo aakulu.+  Pali chinachake chomvetsa chisoni chimene ine ndaona padziko lapansi pano, cholakwa+ chimene amachita wolamulira:+  Zitsiru zaikidwa pa maudindo ambiri akuluakulu,+ koma anthu oyenerera amangokhala pamalo otsika.  Ndaonapo antchito atakwera pamahatchi,* koma akalonga akuyenda pansi ngati antchito.+  Amene akukumba dzenje adzagweramo,+ ndipo amene akugumula mpanda wamiyala njoka idzamuluma.+  Amene akuphwanya miyala, adzadzipweteka nayo, ndipo amene akuwaza nkhuni aziwaza mosamala.+ 10  Ngati nkhwangwa yabuntha ndipo munthu sanainole,+ adzawononga mphamvu zake pachabe. Choncho kugwiritsa ntchito bwino nzeru kumapindulitsa.+ 11  Njoka ikaluma munthu asanaiimbire nyimbo kuti aiseweretse,+ ndiye kuti palibe phindu kwa munthu woimba ndi lilime lakeyo. 12  Mawu a m’kamwa mwa munthu wanzeru amakhala osangalatsa,+ koma milomo ya munthu wopusa imamuwononga.+ 13  Chiyambi cha mawu a m’kamwa mwake ndi uchitsiru,+ ndipo mapeto a mawu a m’kamwa mwake ndi misala yomvetsa chisoni. 14  Ndipo chitsiru chimalankhula mawu ambiri.+ Munthu sadziwa chimene chidzachitike, ndipo ndani angamuuze zimene zidzachitike iye atafa?+ 15  Ntchito imene opusa amagwira mwakhama imawatopetsa,+ chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe amene akudziwa njira yopitira mumzinda.+ 16  Dziko iwe, kodi zidzakuthera bwanji ngati mfumu yako ili kamnyamata,+ ndipo akalonga ako amangokhalira kudya ngakhale m’mawa? 17  Dziko iwe, ndiwe wodala ngati mfumu yako ili mwana wochokera ku banja lachifumu, ndipo akalonga ako amadya pa nthawi yake kuti akhale amphamvu, osati kumangomwa mopitirira muyezo.+ 18  Chifukwa cha ulesi waukulu denga* limaloshoka, ndipo chifukwa cha kuchita manja lende nyumba imadontha.+ 19  Chakudya chimachititsa antchito kuseka, ndipo vinyo amachititsa moyo kusangalala,+ koma ndalama zimathandiza pa zinthu zonse.+ 20  Ngakhale m’chipinda chako, usanenere mfumu zoipa,+ ndipo m’zipinda zimene umagona usanenere zoipa aliyense wolemera,+ chifukwa cholengedwa chouluka chikanena mawu ako ndipo chinachake chokhala ndi mapiko chikaulula zimene wanena.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
Kapena kuti, “tsindwi.”