Malaki 4:1-6

4  “Taonani! Tsiku loyaka ngati ng’anjo likubwera,+ ndipo anthu onse odzikuza ndi onse ochita zoipa adzakhala ngati mapesi.+ Tsiku limene likubweralo lidzawanyeketsa moti pa iwo sipadzatsala mizu kapena nthambi,”+ watero Yehova wa makamu.  “Koma inu amene mukuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakuwalirani+ ndipo m’mapiko mwake mudzakhala mphamvu yochiritsa.+ Inu mudzanyamuka ndi kudumphadumpha ngati ana a ng’ombe amphongo onenepa.”+  “Anthu inu mudzapondaponda anthu oipa. Iwo adzakhala ngati fumbi kumapazi anu pa tsiku limene ndidzachitepo kanthu,”+ watero Yehova wa makamu.  “Anthu inu kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga. Kumbukirani malamulo ndi zigamulo zimene ndinam’patsa ku Horebe zokhudza Aisiraeli onse.+  “Tamverani anthu inu! Tsiku la Yehova lalikulu ndi lochititsa mantha lisanafike,+ ndidzakutumizirani mneneri Eliya.+  Iye adzatembenuza mitima ya abambo kuti ikhale ngati ya ana, ndipo adzatembenuza mitima ya ana kuti ikhale ngati ya abambo.* Adzachita zimenezi kuti ine ndisabwere kudzawononga dziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Iye adzatembenuza mtima wa abambo kuubwezera kwa ana, ndi mtima wa ana kubwezera kwa abambo.”