Malaki 1:1-14

1  Uthenga wokhudza Isiraeli: Nawa mawu a Yehova+ onena za Isiraeli kudzera mwa Malaki:  Yehova wanena kuti: “Ine ndimakukondani anthu inu.”+ Koma inu mwanena kuti: “Mumatikonda motani?”+ “Kodi Esau sanali m’bale wake wa Yakobo?+ Koma ine ndinakonda Yakobo,”+ watero Yehova.  “Esau+ ndinadana naye. Pamapeto pake, mapiri ake ndinawasandutsa bwinja.+ Malo ake okhala, ine ndinawasandutsa malo okhala mimbulu ya m’chipululu.”+  “Popeza kuti Edomu akunena kuti, ‘Ife tawonongedwa, koma tibwerera ndi kukamanga malo athu owonongedwawo,’ Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Iwo akamanga, koma ine ndikagwetsa.+ Anthu adzatcha malo awowo, “dera la zoipa” ndipo iwowo adzatchedwa, “anthu okanidwa ndi Yehova+ mpaka kalekale.”*  Inu mudzaona zimenezi ndi maso anu ndipo mudzati: “Yehova atamandike m’dera lonse la Isiraeli.”’”+  “‘Mwana amalemekeza bambo ake+ ndipo wantchito amalemekeza mbuye wake.+ Ngati ine ndili atate,+ ulemu wanga uli kuti?+ Ngati ndili Ambuye Wamkulu, n’chifukwa chiyani simundiopa?’+ watero Yehova wa makamu kwa inu ansembe amene mukunyoza dzina langa.+ “‘Inu mukunena kuti: “Kodi dzina lanu talinyoza motani?”’  “‘Mwalinyoza mwa kupereka nsembe zodetsedwa paguwa langa lansembe.’+ “‘Inu mukunena kuti: “Takudetsani motani?”’ “‘Mwandidetsa ponena kuti: “Tebulo+ la Yehova ndi lonyozeka.”+  Mukapereka nsembe nyama yakhungu, mumanena kuti: “Palibe cholakwika.” Mukapereka nsembe nyama yolumala kapena yodwala, mumanena kuti: “Palibe cholakwika.”’”+ “Pitani nayo kwa bwanamkubwa wanu. Kodi akakondwera nanu? Kapena kodi akakulandirani bwino?” watero Yehova wa makamu.  “Tsopano khazikani pansi mtima+ wa Mulungu kuti atichitire chifundo.+ Mukuchita zoipazi ndi manja anu. Kodi Mulungu angalandire aliyense wa inu?” watero Yehova wa makamu. 10  “Ndani pakati panu amene angatseke zitseko za kachisi popanda malipiro?+ Anthu inu mumayatsa moto paguwa langa lansembe kuti mulandire malipiro.+ Ine sindikukondwera nanu, ndipo nsembe zanu zimene mukupereka monga mphatso sizikundisangalatsa,”+ watero Yehova wa makamu. 11  “Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kumene limalowera, dzina langa lidzakwezeka pakati pa anthu a mitundu ina.+ Kulikonse anthu azidzapereka nsembe zautsi.+ Anthu azidzapereka zopereka kapena kuti mphatso zovomerezeka polemekeza dzina langa.+ Adzachita izi chifukwa dzina langa lidzakhala lokwezeka pakati pa anthu a mitundu ina,”+ watero Yehova wa makamu. 12  “Koma anthu inu mukundinyoza+ mwa kunena kuti, ‘Palibe vuto kudetsa tebulo la Yehova, ndipo zopereka kapena kuti chakudya chimene chili pamenepo n’chonyozeka.’+ 13  Inu mumanena kuti, ‘Koma ndiye n’zotopetsa bwanji!’+ Ndipo mumanunkhiza nsembezo monyansidwa,” watero Yehova wa makamu. “Inu mumabweretsa nyama zobedwa, zolumala ndi zodwala.+ Mumapereka zimenezi ngati mphatso. Kodi zopereka zanu zoterezi ine ndingakondwere nazo?”+ watero Yehova. 14  “Aliyense wochita zachinyengo popereka nsembe nyama yachilema ndi wotembereredwa. Iye amalonjeza ndi kupereka nsembe nyama yachilema kwa Yehova pamene nyama yamphongo yabwinobwino, ali nayo pagulu la ziweto zake.+ Ine ndine Mfumu yaikulu+ ndipo dzina langa lidzaopedwa pakati pa anthu a mitundu ina,”+ watero Yehova wa makamu.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.