Hoseya 9:1-17

9  “Usasangalale iwe Isiraeli.+ Usachite zinthu mokondwera ngati mitundu ina ya anthu,+ pakuti wasiya Mulungu wako chifukwa cha dama.+ Ukukonda kulandira ndalama za uhule wako pamalo onse opunthira mbewu.+  Malo opunthira mbewu ndiponso oponderamo mphesa sakukupatsa chakudya,+ ndipo vinyo wotsekemera akukukhumudwitsa.+  Iwe sudzapitiriza kukhala m’dziko la Yehova.+ Efuraimu adzabwerera ku Iguputo+ ndipo adzadya zinthu zodetsedwa kudziko la Asuri.+  Iye sadzapitiriza kupatsa Yehova nsembe zavinyo.+ Mulungu sadzakondwera ndi nsembe zake,+ chifukwa zili ngati chakudya cha pamaliro.+ Onse amene adzadya chakudyacho adzadziipitsa. Chakudya chawo chidzakhala chongokhutitsa iwowo basi, ndipo sichidzalowa m’nyumba ya Yehova.+  Kodi anthu inu mudzachita chiyani pa tsiku la msonkhano ndi pa tsiku la chikondwerero cha Yehova?+  Inutu mudzachoka chifukwa dzikolo lidzasakazidwa.+ Anthu a ku Iguputo adzakusonkhanitsani pamodzi+ ndipo anthu a ku Mofi+ adzakuikani m’manda. Zomera zoyabwa zidzamera pakatundu wanu wabwino wasiliva.+ M’mahema mwanu mudzamera zitsamba zaminga.+  “Masiku oti uyenderedwe adzafika,+ masiku oti ulipire adzakwana+ ndipo anthu a Isiraeli adzadziwa zimenezi.+ Mneneri adzapusa+ ndipo munthu wolankhula mawu ouziridwa adzalusa, chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako+ ndiponso chifukwa cha kuchuluka kwa chidani.”  Pa nthawi ina, mlonda+ wa Efuraimu anali ndi Mulungu wanga.+ Koma tsopano panjira zonse za mneneri,+ pali msampha wa wosaka mbalame.+ M’nyumba ya Mulungu wake muli chidani chachikulu.  Aisiraeli azama nazo zinthu zowononga+ ngati m’masiku a Gibeya.+ Mulungu adzakumbukira zolakwa zawo+ ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo. 10  “Isiraeli ndinamupeza ali ngati mphesa zam’chipululu.+ Ndinaona makolo a anthu inu ali ngati nkhuyu zoyambirira pamtengo wa mkuyu wongoyamba kumene kubereka.+ Iwo anapita kwa Baala wa ku Peori+ ndipo anadzipereka kwa chinthu chochititsa manyazicho.+ Anakhala onyansa ngati chinthu chimene anali kuchikondacho.+ 11  Ulemerero wa Efuraimu udzauluka ngati mmene imaulukira mbalame,+ moti sipadzakhalanso kubereka, kukhala ndi pakati, kapena kutenga pakati.+ 12  Pakuti ngakhale alere ana awo, ine ndidzawaphera anawo moti sadzakula n’kukhala amuna.+ Tsoka kwa iwo ndikadzawachokera!+ 13  Efuraimu ndamuona akuoneka ngati Turo atabzalidwa pamalo odyetserapo ziweto a msipu wobiriwira.+ Koma iye adzapititsa ana ake kokaphedwa.”+ 14  Inu Yehova, apatseni zimene mukuyenera kuwapatsa.+ Chititsani kuti mimba zawo zizipita padera+ ndiponso mabere awo afote. 15  “Zoipa zawo zonse zinachitikira ku Giligala,+ ndipo ndinadana nawo kwambiri kumeneko.+ Chifukwa cha zochita zawo zoipa, ndidzawathamangitsa panyumba yanga.+ Sindidzapitiriza kuwakonda.+ Akalonga awo onse akuchita makani.+ 16  Efuraimu adzavulazidwa.+ Muzu wake udzauma,+ ndipo sadzaberekanso chipatso chilichonse.+ Komanso ngati angabereke, ndidzapha chipatso chokondedwa cha mimba yawo.”+ 17  Mulungu wanga+ adzawakana chifukwa sanamumvere,+ ndipo iwo adzakhala othawa kwawo pakati pa mitundu ina.+

Mawu a M'munsi