Hoseya 8:1-14

8  “Ika lipenga la nyanga ya nkhosa pakamwa pako ndipo ulilize.+ Mdani akubwera ngati chiwombankhanga+ kudzaukira nyumba ya Yehova. Akubwera chifukwa Aisiraeli aphwanya pangano langa+ ndiponso aphwanya malamulo anga.+  Iwo akundilirira kuti, ‘Inu Mulungu wathu, ife Aisiraeli tikukudziwani.’+  “Aisiraeli asiya kuchita zabwino,+ chotero mdani awathamangitse.+  Iwo aika mafumu,+ koma osati mwa kufuna kwanga. Aika akalonga, popanda ine kuvomereza. Adzipangira mafano+ pogwiritsa ntchito siliva ndi golide wawo ndipo zimenezi zidzawawonongetsa.+  Iwe Samariya, fano lako la mwana wa ng’ombe latayidwa.+ Mkwiyo wanga wayakira anthu ako.+ Kodi iwo adzalephera kudziyeretsa ku tchimo lawoli mpaka liti?+  Zimenezi zachokera ku Isiraeli.+ Mmisiri ndiye anapanga fano la mwana wa ng’ombe la ku Samariya.+ Fanolo si Mulungu woona, chifukwa lidzangokhala ngati nkhuni zowazawaza.+  “Iwo akungofesa mphepo, ndipo adzakolola mphepo yamkuntho.+ Tirigu amene ali m’minda yawo sakukula.+ Mbewu zawo sizikuwapatsa ufa.+ Ngati zina mwa mbewuzo zingabereke, alendo adzazimeza.+  “Aisiraeli adzamezedwa+ moti adzakhala pakati pa mitundu ina ya anthu+ ngati chiwiya chosasangalatsa.+  Iwo apita kudziko la Asuri+ ngati mbidzi yoyenda yokha.+ Koma Efuraimu walipira akazi kuti azigona nawo.+ 10  Ngakhale kuti akulipira akazi ochokera m’mitundu ina,+ ine ndidzasonkhanitsa anthu pamodzi. Kwa kanthawi, iwo adzamva ululu woopsa+ chifukwa cha katundu wolemetsa amene mafumu ndi akalonga asenzetsa anthu. 11  “Efuraimu wachulukitsa maguwa ansembe ndipo wachimwa.+ Iye wakhala ndi maguwa ansembe ndipo wawonjezera machimo ake.+ 12  Ine ndinamulembera zinthu zambiri zokhudza malamulo anga,+ koma anangoziona ngati zinthu zachilendo.+ 13  Iwo anali kupereka nsembe zanyama ngati mphatso kwa ine+ ndipo anali kuzidya, koma ine Yehova sindinakondwere nazo.+ Tsopano ndidzakumbukira zolakwa zawo. Ndidzawaimba mlandu chifukwa cha machimo awo+ ndiponso chifukwa chakuti iwo anabwerera ku Iguputo.+ 14  Isiraeli anaiwala amene anamupanga+ ndipo anayamba kumanga akachisi.+ Yuda nayenso anachulukitsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+ Koma ine ndidzatumiza moto m’mizinda yake ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za mumzinda uliwonse.”+

Mawu a M'munsi