Hoseya 7:1-16

7  “Nthawi zonse ndikafuna kuchiritsa Isiraeli,+ zolakwa za Efuraimu ndi zoipa za Samariya+ zimaonekera.+ Iwo amachita zachinyengo+ ndipo anthu akuba amalowa m’nyumba komanso gulu la achifwamba limasakaza zinthu panja.+  Mumtima mwawo saganiza+ kuti ine ndidzakumbukira zochita zawo zonse zoipa.+ Tsopano ntchito zawo zawazungulira+ ndipo zili pamaso panga.+  Iwo amasangalatsa mfumu ndi zoipa zawo, ndiponso amasangalatsa akalonga ndi chinyengo chawo.+  Anthu onsewo ndi achigololo.+ Ali ngati ng’anjo yamoto imene wophika mkate waiyatsa. Ng’anjoyo yatentha kwambiri moti iye sakufunikira kuisonkhezera pamene akukanda ufa ndi kudikira kuti ufufume.  Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu, akalonga adzidwalitsa+ ndipo ali ndi ukali chifukwa cha vinyo.+ Mfumuyo yatambasula dzanja lake pamodzi ndi anthu onyoza.  Anthuwo atenthetsa mitima yawo ngati kuti aibweretsa pafupi ndi ng’anjo yamoto.+ Mitima yawoyo ikutentha mkati mwawo.+ Wophika mkate akugona usiku wonse. Pofika m’mawa, ng’anjoyo ikuyaka moto walawilawi.+  Onsewo akutentha ngati ng’anjo yamoto, ndipo akuwononga oweruza awo. Mafumu awo onse agwa.+ Palibe aliyense wa iwo amene akundiitana.+  “Efuraimu amagwirizana ndi anthu a mitundu ina.+ Iye wakhala ngati mkate wozungulira umene wapsa mbali imodzi yokha.+  Alendo alanda mphamvu zake,+ ndipo iye sakudziwa zimenezi.+ Mutu wake wonse wangoti mbuu ndi imvi, koma iye sakudziwa zimenezi. 10  Kunyada kwa Isiraeli kwakhala umboni womutsutsa,+ koma iwo sanabwerere kwa Yehova Mulungu wawo.+ Sanamufunefune ngakhale kuti achita zinthu zonsezi.+ 11  Efuraimu ali ngati nkhunda yopusa,+ yopanda nzeru.+ Iwo apempha thandizo ku Iguputo+ ndiponso apita kudziko la Asuri.+ 12  “Kulikonse kumene iwo angapite, ndidzawatchera ndi ukonde.+ Ndidzawagwira ngati zolengedwa zouluka m’mlengalenga.+ Ndidzawalanga mogwirizana ndi chenjezo limene ndinauza msonkhano wawo.+ 13  Tsoka kwa iwo+ chifukwa andithawa!+ Adzawonongedwa chifukwa chakuti aphwanya malamulo anga. Ine ndinali kufuna kuwawombola,+ koma iwo alankhula mabodza otsutsana nane.+ 14  Sanapemphe thandizo kwa ine ndi mtima wawo wonse+ ngakhale kuti anali kulira mofuula ali pamabedi awo. Anali kungokhala, osachita chilichonse, chifukwa anali ndi chakudya chambiri ndi vinyo wambiri wotsekemera.+ Nthawi zonse anali kuchita zinthu zonditembenukira.+ 15  Ine ndinawalangiza+ ndipo ndinalimbitsa manja awo.+ Koma iwo anali kukonza ziwembu, chotero anakhala otsutsana nane.+ 16  Anabwerera, koma sanapite ku chipembedzo choona.+ Anakhala ngati uta wosakungika.+ Akalonga awo adzaphedwa ndi lupanga chifukwa cha mwano wa lilime lawo lomwe.+ N’chifukwa chake iwo adzanyozedwa m’dziko la Iguputo.”+

Mawu a M'munsi