Hoseya 6:1-11

6  “Bwerani anthu inu. Tiyeni tibwerere kwa Yehova,+ pakuti iye watikhadzulakhadzula+ koma adzatichiritsa.+ Wakhala akutivulaza koma adzamanga zilonda zathu.+  Iye adzatikhalitsa ndi moyo pambuyo pa masiku awiri.+ Pa tsiku lachitatu adzatidzutsa ndipo tidzakhalanso ndi moyo pamaso pake. +  Ife tidzamudziwa Yehova ndipo tidzayesetsa kuti timudziwe bwino.+ N’zosakayikitsa kuti iye adzafika ndithu ngati mmene m’bandakucha+ umafikira.+ Adzabwera kwa ife ngati mvula yambiri.+ Adzabwera ngati mvula yomalizira imene imanyowetsa kwambiri nthaka ya padziko lapansi.”+  “Kodi ndikuchite chiyani iwe Efuraimu? Nanga iwe Yuda, ndikuchite chiyani?+ Anthu inu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kofanana ndi mitambo ya m’mawa, ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma.  N’chifukwa chake anthu amenewa ndidzawasema pogwiritsa ntchito aneneri.+ Ndidzawapha ndi mawu a m’kamwa mwanga.+ Chiweruzo chimene mudzalandire chidzakhala choonekera kwa anthu onse ngati kuwala.+  Pakuti ndimakondwera ndi kukoma mtima kosatha,+ osati ndi nsembe.+ Ndimakondweranso ndi kudziwa Mulungu, osati ndi nsembe zopsereza zathunthu.+  Koma iwo, mofanana ndi munthu wochokera kufumbi, aphwanya pangano.+ Andichitira zachinyengo kumalo kumene amakhala.+  Giliyadi+ ndi tauni ya anthu ochita zinthu zopweteka anzawo, ndipo akhetsa magazi ambiri.+  Gulu la ansembe lakhala gulu la achifwamba.+ Iwo amachita zinthu zofanana ndi za anthu obisalira munthu panjira.+ Amapha anthu m’mphepete mwa njira ku Sekemu+ chifukwa amangokhalira kuchita khalidwe lotayirira.+ 10  Ndaona zinthu zoopsa m’nyumba ya Isiraeli.+ Efuraimu akuchita dama mmenemo.+ Isiraeli wadziipitsa.+ 11  Koma inu anthu a ku Yuda, nthawi yoti musonkhanitsidwe ngati pa nthawi yokolola yakhazikitsidwa. Ine ndidzasonkhanitsanso anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.”+

Mawu a M'munsi