Hoseya 4:1-19

4  Tamverani mawu a Yehova inu ana a Isiraeli. Yehova ali ndi mlandu ndi anthu okhala m’dzikoli,+ chifukwa m’dzikoli mulibe choonadi,+ kukoma mtima kosatha, ndiponso anthu a m’dzikoli amachita zinthu ngati kuti sadziwa Mulungu.+  Kutembererana,+ kuchita zachinyengo,+ kuphana,+ kuba,+ ndi chigololo+ zafala m’dzikoli, ndipo kukhetsa magazi kukuchitika motsatizanatsatizana.+  N’chifukwa chake dzikoli lidzalira maliro+ ndipo aliyense wokhala mmenemo adzalefukiratu pamodzi ndi zilombo zakutchire ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga. Nsomba zam’nyanja nazonso zidzafa.+  “Komabe, munthu asatsutse+ kapena kudzudzula anthu amenewa, chifukwa anthu a mtundu wako ali ngati munthu wotsutsana ndi wansembe.+  Anthu inu mudzapunthwa masana+ ngati kuti ndi usiku. Ngakhalenso mneneri adzapunthwa pamodzi nanu,+ ndipo mayi wanu ndidzamuwononga.+  Anthu anga adzawonongedwa chifukwa sakundidziwa.+ Popeza iwo akana kundidziwa,+ inenso ndidzawakana kuti azinditumikira ngati wansembe wanga.+ Popeza iwo aiwala lamulo la ine Mulungu wawo,+ inenso ndidzaiwala ana awo.+  Pamene iwo achuluka, m’pamenenso akundichimwira kwambiri.+ M’malo mondipatsa ulemu, akundinyoza.+  Iwo akupindula ndi machimo a anthu anga, ndipo amalakalaka tchimo la anthuwo.+  “Zimene zidzachitikira anthuwo zidzachitikiranso ansembe.+ Ndidzawaimba mlandu onsewa chifukwa cha njira zawo+ ndipo ndidzawabwezera zochita zawo.+ 10  Iwo adzadya koma sadzakhuta.+ Adzachita zachiwerewere ndi akazi koma sadzachulukana+ chifukwa chakuti asiya kumvera Yehova.+ 11  Dama, vinyo wakale ndi vinyo wotsekemera zimawononga nzeru za munthu.+ 12  Anthu anga amafunsira zinthu kwa mafano+ awo amtengo+ ndipo ndodo za m’manja mwawo zimawauza zochita. Amachita zimenezi chifukwa chakuti mtima wadama wawasocheretsa+ ndipo asiya kugonjera Mulungu wawo chifukwa cha damalo.+ 13  Iwo amapereka nsembe pamwamba pa mapiri+ ndipo amafukiza nsembe zautsi pazitunda.+ Amachitanso zimenezi pansi pa zimitengo zikuluzikulu, mitengo ya mlanje, ndi mitengo yaikulu, chifukwa ili ndi mthunzi wabwino.+ N’chifukwa chake ana anu aakazi amachita dama ndipo apongozi anu aakazi amachita chigololo. 14  “Sindidzalanga ana anu aakazi chifukwa chakuti akuchita dama, kapenanso apongozi anu aakazi chifukwa chakuti akuchita chigololo, pakuti amuna akumatengana ndi mahule+ ndipo akumaperekera nsembe limodzi ndi mahule aakazi a pakachisi.+ N’chifukwa chake anthu osamvetsa zinthuwa adzapondedwapondedwa.+ 15  Ngakhale kuti inu Aisiraeli mukuchita dama,+ Yuda asakhale wolakwa+ ndipo anthu inu musabwere ku Giligala.+ Musapitenso ku Beti-aveni+ kapena kulumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo!’+ 16  Isiraeli wakhala wamakani* ngati ng’ombe yamakani.+ Choncho kodi Yehova angawawete ngati nkhosa yamphongo yaing’ono pamalo otakasuka? 17  Efuraimu wagwirizana ndi mafano.+ Musiyeni aona!+ 18  Popeza mowa wawo watha,+ ayamba kuchita zachiwerewere ndi akazi.+ Oteteza+ anthu m’dzikolo akukonda zinthu zochititsa manyazi.+ 19  Mphepo yawakulunga m’mapiko ake,+ ndipo iwo adzachita manyazi ndi nsembe zawo.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “wanthota.”