Hoseya 3:1-5

3  Yehova anandiuza kuti: “Yambanso kukonda mkazi wokondedwa ndi mwamuna,+ mkazi amene akuchita chigololo. Ukamukonde ngati mmene Yehova akukondera ana a Isiraeli,+ ngakhale kuti iwo akutembenukira kwa milungu ina,+ imene amakonda kuipatsa nsembe za mphesa zouma zoumba pamodzi.”+  Chotero ndinagula mkaziyo ndi ndalama zasiliva 15+ ndi balere wokwana muyezo umodzi wa homeri* ndi hafu.  Kenako ndinamuuza kuti: “Ukhala ndi ine masiku ambiri.+ Usachite dama+ ndipo usagone ndi mwamuna wina.+ Inenso sindigona nawe.”  Ziyenera kukhala choncho chifukwa chakuti kwa masiku ambiri, ana a Isiraeli adzakhala opanda mfumu,+ kalonga, nsembe,+ chipilala chopatulika, efodi,+ ndi aterafi.*+  Kenako ana a Isiraeli adzabwerera ndi kufunafuna Yehova Mulungu wawo+ ndiponso Davide mfumu yawo.+ Iwo adzabwera kwa Yehova akunjenjemera+ ndipo adzafunafuna ubwino wake m’masiku otsiriza.+

Mawu a M'munsi

“Homeri” imodzi ndi yofanana ndi malita 220.
“Aterafi” ndi milungu kapena mafano amene mabanja anali kupembedza.