Hoseya 14:1-9

14  “Iwe Isiraeli, bwerera kwa Yehova Mulungu wako+ pakuti wapunthwa mu zolakwa zako.+  Bwerera kwa Yehova ndi mawu osonyeza kulapa.+ Anthu nonsenu uzani Mulungu kuti, ‘Tikhululukireni zolakwa zathu.+ Landirani zinthu zabwino zochokera kwa ife, ndipo mawu apakamwa pathu akhale ngati ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe kwa inu.+  Dziko la Asuri silidzatipulumutsa.+ Ife sitidzakwera pamahatchi.+ Sitidzauzanso ntchito ya manja athu kuti: “Inu Mulungu wathu!” chifukwa inu mumachitira chifundo mwana wamasiye.’*+  “Ndidzathetsa kusakhulupirika kwawo.+ Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga,+ chifukwa mkwiyo wanga wawachokera.+  Ine ndidzakhala ngati mame kwa Isiraeli,+ ndipo iye adzaphuka ngati maluwa okongola. Mizu yake idzazama ngati mtengo wa ku Lebanoni.  Nthambi zake zidzaphukira ndipo adzakhala ndi ulemerero ngati mtengo wa maolivi.+ Fungo lake lonunkhira lidzakhala ngati mtengo wa ku Lebanoni.  Iwo adzakhalanso mumthunzi wake.+ Adzabzala mbewu ndipo adzaphuka ngati mpesa.+ Dzina lawo lidzakumbukiridwa ngati vinyo wa ku Lebanoni.  “Efuraimu adzanena kuti, ‘Kodi mafano ndi a chiyaninso kwa ine?’+ “Ine ndidzamva ndipo ndidzapitirizabe kumuyang’anira.+ Ine ndili ngati mtengo waukulu wa mkungudza wamasamba obiriwira+ ndipo mudzapeza zipatso kwa ine.”  Ndani ali ndi nzeru kuti amvetse zinthu zimenezi?+ Wochenjera ndani kuti adziwe zimenezi?+ Pakuti njira za Yehova ndi zowongoka+ ndipo anthu olungama ndi amene adzayendamo,+ koma olakwa adzapunthwa m’njira zimenezo.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”