Hoseya 13:1-16

13  “Efuraimu akalankhula, anthu anali kunjenjemera. Iye anali wolemekezeka mu Isiraeli,+ koma anapezeka ndi mlandu wolambira Baala+ ndipo anafa.+  Tsopano anthu ake akuchita machimo ena ndipo akugwiritsa ntchito siliva wawo popanga zifanizo zachitsulo chosungunula.+ Zifanizo zimenezo ndi mafano opangidwa mogwirizana ndi maganizo awo,+ koma zonsezi ndi ntchito za amisiri.+ Iwo amauza mafanowo kuti, ‘Amuna opereka nsembe apsompsone mafano a ana ang’ombe.’+  Chotero iwo adzakhala ngati mitambo ya m’mawa+ ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma. Adzakhalanso ngati mankhusu* amene amauluzika kuchokera pamalo opunthira mbewu+ ndiponso ngati utsi umene umatuluka m’chumuni kudenga.*  “Koma ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo.+ Panalibe Mulungu wina amene unali kumudziwa kupatulapo ine. Panalibenso mpulumutsi wina kupatulapo ine.+  Ine ndinakudziwa uli m’chipululu,+ m’dziko la matenda otenthetsa thupi.+  Iwe unakhuta chifukwa chakuti unali ndi zakudya zambiri.+ Unakhuta ndipo mtima wako unayamba kudzitukumula.+ N’chifukwa chake unandiiwala.+  Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa iwo.+ Ndidzapitiriza kuwayang’ana ngati kambuku* amene wabisala m’mphepete mwa njira.+  Ndidzawaukira ngati chimbalangondo chimene ana ake asowa+ ndipo ndidzang’amba zifuwa zawo, mmene muli mitima yawo. Ndidzawadya kumeneko ngati mkango.+ Chilombo chakuthengo chidzawakhadzulakhadzula.+  Chifukwa chakuti zimene iwe Isiraeli unachita zinali zotsutsana ndi ine mthandizi wako,+ zimenezo zidzakuwononga.+ 10  “Tsopano mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse m’mizinda yako yonse.+ Oweruza ako ali kuti amene unawauza kuti, ‘Ndipatseni mfumu ndi akalonga’?+ 11  Ndiyeno ndinakupatsa mfumu nditakwiya+ ndipo ndidzaichotsa nditakwiya.+ 12  “Zolakwa za Efuraimu zakulungidwa pamodzi, ndipo machimo ake asungidwa.+ 13  Zowawa ngati za mkazi amene akubereka zidzamugwera.+ Iye ndi mwana wopanda nzeru+ chifukwa nthawi yoti abadwe ikakwana, sadzadziika pamalo amene ana amatulukira pochokera m’chiberekero.+ 14  “Ine ndidzawawombola ku Manda*+ ndiponso ku imfa.+ Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?+ Iwe Manda amene umawononga, kodi uli kuti?+ Koma Efuraimu sindimumverabe chisoni.+ 15  “Ndipo iye akayamba kubereka ndi kutulutsa ana ngati bango,+ mphepo ya kum’mawa, mphepo ya Yehova idzabwera.+ Mphepo yake ikuchokera kuchipululu ndipo idzaumitsa chitsime chake ndi kuphwetsa kasupe wake.+ Ameneyo adzawononga chuma chimene chikuphatikizapo zinthu zosiririka.+ 16  “Samariya adzaimbidwa mlandu+ chifukwa iye akupandukira Mulungu wake.+ Iwo adzagwetsedwa ndi lupanga.+ Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa+ ndipo akazi awo amene ali ndi pakati adzatumbulidwa.”+

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Kapena kuti “tsindwi.”
Ena amati “nyalugwe.”
Onani Zakumapeto 5.