Hoseya 12:1-14

12  “Efuraimu akudya mphepo+ ndi kuthamangitsa mphepo ya kum’mawa tsiku lonse.+ Iye akuchulukitsa mabodza ndipo akuwononga zinthu zambiri.+ Wachita pangano ndi Asuri+ ndipo wapititsa mafuta ku Iguputo.  “Yehova ali ndi mlandu woti aimbe Yuda.+ Adzalanga Yakobo mogwirizana ndi njira zake+ ndipo adzamubwezera mogwirizana ndi zochita zake.+  Pamene Yakobo anali m’mimba anagwira m’bale wake chidendene.+ Iye analimbana ndi Mulungu ndi mphamvu zake zonse.+  Anapitiriza kulimbana ndi mngelo ndipo pamapeto pake anapambana.+ Analira pochonderera kuti amudalitse.”+ Mulungu anamupeza ku Beteli+ ndipo kumeneko Mulungu anayamba kulankhula nafe.+  Iye ndi Yehova Mulungu wa makamu.+ Yehova ndilo dzina lake lomukumbukira nalo.+  “Koma iwe ubwerere kwa Mulungu wako.+ Usonyeze kukoma mtima kosatha+ ndi chilungamo+ ndipo nthawi zonse uziyembekezera Mulungu wako.+  M’manja mwa wamalonda muli sikelo yachinyengo+ ndipo iye amakonda kuba mwachinyengo.+  Efuraimu akupitiriza kunena kuti, ‘Inetu ndalemeradi,+ ndapeza zinthu zamtengo wapatali.+ Palibe amene angapeze cholakwa chachikulu pa ntchito zanga zonse.’+  “Ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo.+ Koma ndidzakuchititsa kukhala m’mahema ngati pa masiku achikondwerero. 10  Ndinalankhula ndi aneneri+ ndipo ndinawaonetsa masomphenya ochuluka. Kudzera mwa aneneri, ndinali kupereka mafanizo ambiri.+ 11  “Ku Giliyadi anthu akuchita zamatsenga+ ndiponso akulankhula zabodza.+ Ku Giligala akupereka nsembe ng’ombe zamphongo.+ Komanso maguwa awo ansembe ali ngati milu ya miyala m’mizere ya m’munda.+ 12  Yakobo anathawira kumunda wa ku Siriya+ ndipo Isiraeli+ anapitirizabe kugwira ntchito+ ndi kulondera nkhosa kuti apeze mkazi.+ 13  Yehova anatulutsa Isiraeli ku Iguputo pogwiritsa ntchito mneneri,+ ndipo mneneri analondera Isiraeli.+ 14  Efuraimu anakhumudwitsa kwambiri Mulungu.+ Magazi amene iye anakhetsa ali pa iyeyo+ ndipo Ambuye Wamkulu adzamubwezera chitonzo chake.”+

Mawu a M'munsi