Hoseya 10:1-15

10  “Isiraeli ndi mtengo wa mpesa umene ukuwonongeka.+ Iye akupitiriza kubereka zipatso+ ndipo wachulukitsa maguwa ansembe mogwirizana ndi kuchuluka kwa zipatso zake.+ Pamene dzikolo likutukuka kwambiri m’pamenenso Aisiraeli akumanga zipilala zopatulika zokongola kwambiri.+  Mtima wawo wakhala wachinyengo.+ Tsopano iwo adzapezeka ndi mlandu. “Pali wina amene adzathyola maguwa awo ansembe ndipo adzasakaza zipilala zawo zopatulika.+  Ndiyeno iwo adzanena kuti, ‘Tilibe mfumu+ pakuti sitinaope Yehova. Ngakhale tikanakhala ndi mfumu, kodi ikanatichitira chiyani?’  “Iwo amalankhula mawu opanda pake, amachita malumbiro abodza,+ amachita mapangano+ ndipo kusalungama kwafalikira ngati zomera zakupha m’mizere ya m’munda.+  Anthu okhala ku Samariya adzachita mantha ndi fano la ku Beti-aveni+ la mwana wa ng’ombe. Pakuti anthuwo pamodzi ndi ansembe a mulungu wachilendo, amene anali kusangalala ndi fanolo chifukwa cha ulemerero wake, adzalilirira. Adzalirira fanolo chifukwa ulemerero wake udzachoka likadzatengedwa kupita kudziko lina.+  Wina adzapititsa fanolo kudziko la Asuri ndi kukalipereka monga mphatso kwa mfumu yaikulu.+ Efuraimu adzachita manyazi+ ndipo Isiraeli adzachita manyazi ndi zoipa zimene anali kufuna kuchita.+  Samariya pamodzi ndi mfumu yake adzakhalitsidwa chete,+ ngati kanthambi kothyoledwa mumtengo kamene kakuyandama pamadzi.  Malo okwezeka a ku Beti-aveni,+ omwe ndi tchimo la Isiraeli,+ adzawonongedwa. Minga ndi zitsamba zobaya*+ zidzamera pamaguwa awo ansembe.+ Anthu adzauza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza zitunda kuti, ‘Tikwirireni!’+  “Inu ana a Isiraeli, mwakhala mukuchimwa kuyambira m’masiku a Gibeya+ ndipo anthu anapitirizabe kuchita machimo kumeneko. Nkhondo ya ku Gibeya yomenyana ndi anthu osalungama sinawawononge onse.+ 10  Ndidzawalanga mtima wanga ukadzafuna.+ Anthu a mitundu ina adzasonkhana kuti alimbane nawo pa nthawi imene iwo adzamangidwe kugoli la zolakwa zawo ziwiri.+ 11  “Efuraimu anali ng’ombe yaikazi yosaberekapo yophunzitsidwa bwino yokonda kupuntha mbewu,+ ndipo ine ndinapitirira khosi lake lokongola. Koma tsopano ndichititsa wina kukwera pamsana pa Efuraimu.+ Yuda akulima,+ Yakobo akumusalazira zibuma za dothi.+ 12  Bzalani mbewu za chilungamo+ ndipo kololani zipatso za kukoma mtima kosatha.+ Limani munda panthaka yabwino+ pamene muli ndi nthawi yofunafuna Yehova, kufikira iye atabwera+ ndi kukupatsani malangizo onena za chilungamo.+ 13  “Anthu inu mwalima zoipa+ ndipo mwakolola kusalungama.+ Mwadya zipatso za zochita zanu zachinyengo,+ pakuti munali kudalira njira zanu+ ndi kuchuluka kwa anthu anu amphamvu.+ 14  Pakati pa anthu a mtundu wanu pachitika chisokonezo+ ndipo mizinda yanu yonse yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzawonongedwa,+ ngati mmene Salimani anawonongera Beti-aribeli. Iye anachita zimenezi pa tsiku lankhondo, pamene amayi anaphwanyidwaphwanyidwa pamodzi ndi ana awo.+ 15  Inu anthu a ku Beteli, wina adzakuchitaninso zimenezi chifukwa ndinu anthu oipitsitsa.+ Ndithu, mfumu ya Isiraeli adzaikhalitsa chete m’bandakucha.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “kulasa.”