Hoseya 1:1-11

1  Yehova analankhula+ ndi Hoseya+ mwana wa Beeri m’masiku+ a Uziya,+ Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya+ mafumu a Yuda, ndiponso m’masiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi+ mfumu ya Isiraeli.  M’masiku amenewo, Yehova anayamba kulankhula kudzera mwa Hoseya, ndipo Yehova anauza Hoseya kuti: “Pita+ ukakwatire mkazi amene adzachita dama. Pamenepo udzakhala ndi ana chifukwa cha dama la mkazi wakoyo. Pakuti mwanjira yofanana ndi zimenezi, dzikoli latembenuka ndi kusiya kutsatira Yehova chifukwa cha dama.”+  Pamenepo Hoseya anapita ndi kukakwatira Gomeri, mwana wamkazi wa Dibulaimu. Kenako Gomeri anatenga pakati ndipo anamuberekera mwana wamwamuna.+  Ndiyeno Yehova anauza Hoseya kuti: “Mwanayu umupatse dzina lakuti Yezereeli,+ pakuti kwatsala kanthawi kochepa kuti ndiimbe Yezereeli* mlandu wokhetsa magazi, mlandu wa nyumba ya Yehu.+ Pamenepo ndidzathetsa ufumu wolamulira nyumba ya Isiraeli,+  ndipo m’masiku amenewo ndidzathyola uta+ wa Isiraeli m’chigwa cha Yezereeli.”  Kenako Gomeri anatenganso pakati ndi kubereka mwana wamkazi. Ndiyeno Mulungu anauza Hoseya kuti: “Mwanayu umupatse dzina lakuti Lo-ruhama,*+ pakuti sindidzachitiranso chifundo+ anthu a m’nyumba ya Isiraeli, chifukwa ndidzawathamangitsa.+  Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda,+ ndipo Ine Yehova Mulungu wawo, ndidzawapulumutsa.+ Sindidzawapulumutsa ndi uta, lupanga, nkhondo, mahatchi* kapena ndi amuna okwera pamahatchi ayi.”+  Patapita nthawi, Gomeri anasiyitsa mwana wake Lo-ruhama kuyamwa, ndipo anatenganso pakati ndi kubereka mwana wamwamuna.  Pamenepo Mulungu anati: “Mwanayu umupatse dzina lakuti Lo-ami,* chifukwa anthu inu sindinu anthu anga ndipo ine sindidzakhala Mulungu wanu. 10  “Ndiyeno ana a Isiraeli adzachuluka ngati mchenga wakunyanja umene munthu sangathe kuuyeza kapena kuuwerenga.+ Ndipo kumene anali kuuzidwa kuti, ‘Anthu inu sindinu anthu anga,’+ adzauzidwanso kuti, ‘Inu ndinu ana a Mulungu wamoyo.’+ 11  Pamenepo ana a Yuda ndi ana a Isiraeli adzasonkhanitsidwa pamodzi ndipo adzakhala ogwirizana.+ Iwo adzadziikira mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka m’dzikolo,+ chifukwa tsikuli lidzakhala lofunika kwambiri kwa Yezereeli.*+

Mawu a M'munsi

Umenewu unali mzinda wachifumu kumene mafumu a Isiraeli anali kukhala, ngakhale kuti likulu lawo linali mzinda wa Samariya. Onani 1Mf 21:1.
Dzinali limatanthauza kuti, “Sanamuchitire Chifundo.”
Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
Dzinali limatanthauza kuti, “Iwo Si Anthu Anga.”
Dzinali limatanthauza kuti, “Mulungu Adzafesa Mbewu.”