Hagai 1:1-15
1 M’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo,+ m’mwezi wa 6, pa tsiku loyamba la mweziwo, mawu a Yehova anafika kwa Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ bwanamkubwa wa Yuda,+ ndi kwa Yoswa+ mwana wa Yehozadaki+ mkulu wa ansembe. Mawuwa anafika kwa anthu amenewa kudzera mwa mneneri Hagai+ kuti:
2 “Yehova wa makamu+ wanena kuti, ‘Anthu awa akunena kuti: “Nthawi yomanga nyumba ya Yehova sinakwane.”’”+
3 Yehova anapitiriza kulankhula kudzera mwa mneneri Hagai kuti:
4 “Kodi ino ndi nthawi yoti inu muzikhala m’nyumba zokongoletsedwa ndi matabwa,+ nyumba iyi ili bwinja?+
5 Tsopano Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ganizirani mofatsa zimene mukuchita.+
6 Mwafesa mbewu zambiri koma zokolola zanu n’zochepa.+ Mukudya koma simukukhuta.+ Mukumwa koma simukukhutira.* Mukuvala zovala koma simukumva kutentha. Amene akugwira ganyu akulandirira ndalama zake m’matumba obowoka.’”+
7 “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ganizirani mofatsa zimene mukuchita.’+
8 “‘Pitani kuphiri ndipo mukabweretse mitengo yomangira nyumba.+ Mumange nyumbayi+ kuti ndisangalale nayo+ komanso nditamandidwe,’+ watero Yehova.”
9 “‘Munali kufunafuna zinthu zambiri, koma mwapeza zochepa.+ Mwabweretsa zinthuzo m’nyumba zanu ndipo ine ndaziuzira n’kuzimwaza.+ N’chifukwa chiyani ndachita zimenezi?+ Chifukwa chakuti simunamalize kumanga nyumba yanga. Koma aliyense wa inu akuthamangathamanga kuti asamalirire nyumba yake,’+ watero Yehova wa makamu.
10 ‘N’chifukwa chake kumwamba sikunakugwetsereni mame, ndipo dziko lapansi silinakupatseni zipatso zake.+
11 Ndinalamula kuti chilala chigwe padziko lapansi, pamapiri, pambewu, pavinyo watsopano,+ pamafuta, pazinthu zonse zochokera munthaka, pa anthu, paziweto ndi pa ntchito iliyonse ya manja anu.’”+
12 Ndiyeno Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki+ mkulu wa ansembe, ndiponso anthu ena onse anayamba kumvetsera mawu a Yehova Mulungu wawo+ ndi a mneneri Hagai,+ chifukwa Yehova Mulungu wawo anamutuma. Pamenepo anthuwo anayamba kuchita mantha chifukwa cha Yehova.+
13 Hagai mthenga+ wa Yehova analankhula kwa anthuwo malinga ndi ntchito imene Yehova anam’patsa.+ Iye anati: “‘Ine ndili ndi inu,’+ watero Yehova.”
14 Yehova analimbikitsa+ Zerubabele mwana wa Salatiyeli bwanamkubwa wa Yuda, Yoswa+ mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe ndi anthu ena onse. Choncho iwo anapita kukagwira ntchito panyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wawo.+
15 Zimenezi zinachitika pa tsiku la 24 la mwezi wa 6, m’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “simukuledzera.”