Habakuku 3:1-19

3  Ili ndi pemphero la mneneri Habakuku limene anaimba ngati nyimbo yoimba polira:*  “Inu Yehova, ndamva uthenga wonena za inu.+ Ndachita mantha ndi ntchito zanu, Inu Yehova.+ M’zaka zimenezi sonyezani ntchito zanu! m’zaka zimenezi chititsani ntchito zanu kuti zidziwike. Pa nthawi ya mkwiyo wanu kumbukirani kusonyeza chifundo.+  Mulungu anabwera kuchokera ku Temani, Woyerayo anabwera kuchokera kuphiri la Parana.+ [Seʹlah.]+ Ulemerero wake unaphimba kumwamba+ ndipo dziko lonse linamutamanda.+  Kuwala kwake kunali ngati kuwala kwa masana.+ Kuwala kwa mitundu iwiri kunali kutuluka m’dzanja lake ndipo m’dzanja lakemo ndi mmene munali kubisala mphamvu zake.+  Mliri unali kuyenda patsogolo pake+ ndipo matenda otenthetsa thupi anali kuyenda patsogolo pa mapazi ake.+  Iye anaima chilili kuti agwedeze dziko lapansi.+ Anayang’ana mitundu ya anthu ndipo mitunduyo inadumpha.+ Mapiri amuyaya anaphwanyidwa.+ Zitunda zimene zidzakhalapo mpaka kalekale* zinawerama.+ Zimenezi ndi njira zake zakalekale.  Ndinaona mahema a Kusani ali ndi nkhawa. Nsalu za mahema a m’dziko la Midiyani+ zinayamba kunjenjemera.+  Inu Yehova, kodi mwapsera mtima mitsinje?+ Kodi mkwiyo wanu wayakira nyanja+ pamene inu munakwera pamahatchi anu?+ Magaleta anu anabweretsa chipulumutso.+  Munachotsa uta moikamo mwake.+ Zimene mafuko a anthu ananena ndiwo malumbiro awo.+ [Seʹlah.] Munagawa dziko lapansi pogwiritsa ntchito mitsinje.+ 10  Mapiri anakuonani ndipo anamva ululu waukulu.+ Mvula yamphamvu yamabingu inadutsa. Madzi akuya anachita mkokomo+ ndipo anathuvuka m’malere. 11  Kumwamba,+ dzuwa ndi mwezi zinaima.+ Mivi yanu inapitiriza kuyenda ngati kuwala.+ Kunyezimira kwa mkondo wanu kunakhala ngati kuwala kounikira.+ 12  Munadutsa m’dziko lapansi ndi kulidzudzula mwamphamvu. Inu mutakwiya munapuntha mitundu ya anthu ngati mbewu.+ 13  Munapita kuti mukapulumutse anthu anu,+ kuti mukapulumutse wodzozedwa wanu. Munaphwanyaphwanya mtsogoleri wa nyumba ya wochimwa.+ Nyumbayo inafafanizidwa mpaka kudenga moti maziko a nyumbayo anaonekera.+ [Seʹlah.] 14  Munabaya*+ mitu ya asilikali ake ndi zida zake zomwe, pamene iwo anali kubwera ngati mphepo yamkuntho kuti adzandimwaze.+ Kukondwera kwawo chifukwa cha tsoka langa kunali ngati kwa anthu amene akonzeka kuti ameze munthu wosautsidwa m’malo obisalamo.+ 15  Munadutsa panyanja ndi mahatchi anu, munadutsa pamadzi ambiri.+ 16  Nditamva mawu ake, m’mimba mwanga munayamba kubwadamuka ndipo milomo yanga inanjenjemera. Mafupa anga anayamba kuwola+ ndipo ndinanthunthumira chifukwa cha mmene zinthu zinalili. Choncho ndidzayembekezera mofatsa tsiku la nsautso.+ Tsiku limeneli lidzabwera kwa anthu+ ngati mmene munthu amabwerera kwa adani ake kuti awaukire. 17  Ngakhale mkuyu usaphukire maluwa,+ mtengo wa mpesa usabale zipatso, mtengo wa maolivi ulephere kubala zipatso, munda wa m’mphepete mwa phiri usatulutse chakudya,+ nkhosa ndi ng’ombe zithemo m’khola,+ 18  Ine ndidzakondwerabe mwa Yehova+ ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wachipulumutso changa.+ 19  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndiye mphamvu yanga.+ Iye adzachititsa miyendo yanga kukhala ngati ya mbawala,+ moti adzandiyendetsa pamalo anga okwezeka.”+Kwa wotsogolera nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo zanga za zingwe.

Mawu a M'munsi

Tanthauzo la mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “nyimbo yoimba polira” silikudziwika, koma mwina angatanthauze nyimbo yoimba mokhudzika mtima kwambiri. Kaimbidwe kake kangasonyeze kuti moyo wa munthu woimbayo uli pangozi, akufuula kupempha thandizo, kapena akukondwera ndiponso kutamanda winawake.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “kugwaza.”