Habakuku 2:1-20

2  Ine ndidzaimabe+ pamalo a mlonda ndiponso pakhoma lachitetezo. Ndidzakhala tcheru+ kuti ndione uthenga umene iye adzalankhula kudzera mwa ine+ ndi zimene ndidzayankha pamene iye akundidzudzula.+  Pamenepo Yehova anandiyankha kuti: “Lemba masomphenyawa moonekera bwino pamiyala yosema,+ kuti wowerenga mokweza awerenge mosadodoma.+  Uchite zimenezi pakuti masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu+ ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe* chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu.+ Iwo sadzachedwa.  “Taona! Iye wadzitukumula+ ndipo si wowongoka mtima. Koma wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.+  Ndiye pakuti vinyo ndi wachinyengo,+ mwamuna wamphamvu amadzimva,+ koma sadzakwaniritsa cholinga chake.+ Iye wakulitsa chilakolako chake ngati Manda* ndipo sangakhutire ngati imfa.+ Iye akupitiriza kudzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu ndi anthu onse pamodzi.+  Kodi anthu onsewa sadzamunenera mwambi,+ chining’a ndi mawu okuluwika? Wina adzanena kuti,“‘Kodi iye adzapitiriza kuchulukitsa zinthu zimene si zake+ kwa nthawi yaitali bwanji?+ Tsoka kwa iye pakuti akungochulukitsa ngongole yake.  Kodi amene uli nawo ngongole sadzanyamuka ndi kubwera modzidzimutsa kuti uwabwezere ngongole yawo? Kodi okugwedeza mwachiwawa sadzanyamuka ndi kubwera kudzafunkha zinthu zako zonse?+  Chifukwa chakuti iwe unafunkha mitundu yambiri ya anthu, anthu onse otsala a m’mitunduyo adzafunkha zinthu zako.+ Iwo adzateronso chifukwa unakhetsa magazi a mtundu wa anthu komanso unachitira chiwawa dziko lapansi, tauni ndi anthu onse okhala mmenemo.+  “‘Tsoka kwa munthu amene akupezera nyumba yake phindu mwachinyengo.+ Iye akuchita zimenezi kuti amange chisa chake pamalo okwezeka ndi cholinga choti tsoka lisamupeze.+ 10  Wapereka malangizo ochititsa manyazi kunyumba yako, kumene ndi kuphetsa mitundu yambiri ya anthu+ ndipo wachimwa.+ 11  Mwala wa pakhoma* udzalira mwachisoni ndipo kuchokera padenga* mtanda wa denga udzayankha.+ 12  “‘Tsoka kwa munthu amene akumanga mzinda mwa kukhetsa magazi, amenenso wakhazikitsa tauni mwa kuchita zosalungama.+ 13  Taona! Kodi si Yehova wa makamu amene adzachititsa anthu kugwira ntchito yakalavulagaga kuti moto uwononge ntchitoyo? Kodi sindiye amene wachititsa kuti mitundu ya anthu idzitopetse pachabe?+ 14  Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemerero wa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.+ 15  “‘Tsoka kwa amene akupatsa anzake chakumwa kuti amwe, koma atachisakaniza ndi mkwiyo ndiponso kupsa mtima kuti anzakewo aledzere+ ndipo iye aone maliseche awo.+ 16  Iwenso adzakumwetsa+ ndipo udzaonekera kuti ndiwe wosadulidwa.+ Udzakhuta zinthu zamanyazi m’malo mwa ulemerero.+ Chikho chochokera m’dzanja lamanja la Yehova chidzakupeza+ ndipo ulemerero wako udzasanduka manyazi. 17  Zidzakhala choncho chifukwa chiwawa chimene unachitira Lebanoni+ chidzafika pa iwe ndiponso chifukwa cha kuwononga kwako kwakukulu kumene unaopseza nako zilombo zakutchire, kukhetsa magazi a anthu ndi chiwawa chimene unachitira dziko lapansi,+ tauni ndi onse okhala mmenemo.+ 18  Kodi chifaniziro chosema, chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndiponso mphunzitsi wonama,+ zili ndi phindu lanji+ kuti wozipanga azizikhulupirira+ ndipo azipanga milungu yopanda pake yosalankhula?+ 19  “‘Tsoka kwa munthu amene akuuza chidutswa cha mtengo kuti: “Dzuka!” Amene amauzanso mwala wosalankhula kuti: “Dzuka! Tipatse malangizo”!+ Taona! Fanolo ndi lokutidwa ndi golide ndi siliva+ ndipo mulibe mpweya* mkati mwake.+ 20  Koma Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+ Inu anthu onse a padziko lapansi, khalani chete pamaso pake!’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Ngakhale masomphenyawa ataoneka ngati akuchedwa, uziwayembekezerabe.”
Onani Zakumapeto 5.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”
Kapena kuti “patsindwi.”
Onani Zakumapeto 4.