Habakuku 1:1-17

1  Uwu ndi uthenga umene ine, mneneri Habakuku, ndinauzidwa m’masomphenya. Ndinati:  “Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo koma inu osandimva kufikira liti?+ Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku chiwawa koma inu osandimva kufikira liti?+  N’chifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zopweteka? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa? N’chifukwa chiyani kufunkha ndi chiwawa zikuchitika pamaso panga? Ndipo n’chifukwa chiyani pali mikangano ndi kumenyana?+  “Choncho lamulo latha mphamvu ndipo anthu sakuchitanso chilungamo.+ Chilungamo chapotozedwa chifukwa anthu oipa akupondereza anthu olungama.+  “Yang’anani pakati pa mitundu ya anthu ena anthu inu, ndipo muyang’anitsitse, kenako muyang’anane modabwa.+ Dabwani pakuti pali ntchito imene winawake akuichita m’masiku anu imene anthu inu simungakhulupirire ngakhale wina atakufotokozerani.+  Ine ndikuutsa Akasidi,+ mtundu waukali ndi waphuma umene ukupita kumalo otakasuka a padziko lapansi kukatenga malo amene si awo.+  Mtundu umenewu ndi woopsa ndipo anthu amachita nawo mantha. Mtunduwo umapanga malamulo akeake ndipo umadzipezera wokha ulemu.+  Mahatchi* ake ndi aliwiro kuposa akambuku* ndiponso ndi oopsa kuposa mimbulu yoyenda usiku.+ Mahatchi ake ankhondo amachita mgugu ndipo amachokera kutali. Mahatchiwo amauluka ngati chiwombankhanga chimene chikuthamangira chakudya chake.+  Mtunduwo umabwera wonse wathunthu kuti udzachite chiwawa.+ Ukakumana wonse pamodzi umayenda ngati mphepo yamkuntho yochokera kum’mawa,+ ndipo umasonkhanitsa anthu ogwidwa, ochuluka ngati mchenga. 10  Mtunduwu umaseka mafumu monyodola ndipo umaona nduna zapamwamba ngati choseketsa.+ Umasekanso malo alionse okhala ndi mpanda wolimba kwambiri+ ndipo umaunjika dothi kenako n’kulanda malowo. 11  Pa nthawi imeneyo mtunduwo udzayendabe ngati mphepo ndipo udzadutsa m’dzikoli ndi kupalamula.+ Mphamvu zake ndizo mulungu wake.”+ 12  Inu Yehova, inutu mwakhalapo kuyambira kalekale.+ Inu Mulungu wanga, Mulungu wanga Woyera, inu simufa.+ Inu Yehova, mwaika Akasidi pamalo oti muwaweruze. Inu Thanthwe,+ mwasankha kuti mutidzudzule.+ 13  Inu ndinu woyera kwambiri moti simungaonerere zinthu zoipa ndipo simungathe kuonerera khalidwe loipa.+ N’chifukwa chiyani mumayang’ana anthu amene amachita zachinyengo,+ ndipo n’chifukwa chiyani mukupitiriza kukhala chete pamene munthu woipa akumeza munthu amene ndi wolungama kuposa iyeyo?+ 14  N’chifukwa chiyani mukuchititsa munthu kukhala ngati nsomba zam’nyanja ndiponso ngati zokwawa zam’nyanja zimene zilibe mtsogoleri woziteteza?+ 15  Mdani amagwira zonsezi ndi mbedza+ ndipo amazikokolola ndi khoka lake n’kuzisonkhanitsa muukonde wake wophera nsomba.+ N’chifukwa chake iye amasangalala ndipo amakhala wokondwa.+ 16  N’chifukwa chake mdaniyo amaperekera nsembe khoka lake ndipo amafukizira nsembe yautsi ukonde wake wophera nsomba. Iye amatero chifukwa chakuti amapeza chakudya chonona ndiponso chakudya chopatsa thanzi chifukwa cha khoka ndi ukonde wakewo.+ 17  Kodi ndicho chifukwa chake adzapitirizabe kudzaza ndi kukhuthula nsomba za m’khoka lake? Kodi iye adzapitirizabe kupha mitundu ya anthu mopanda chifundo?+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”
Ena amati “nyalugwe.”